Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"TIKUYENERA KUPAMBANA MASEWEROWA" - SIBALE
Mphunzitsi wachiwiri kutimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati timu yake ikuyenera kupambana masewero awo ndi timu ya Karonga United ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligi komwe iwo ali.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe aliko pa bwalo la Karonga lamulungu ndipo wati akudziwa kuti akhale ovuta chifukwa choti Karonga ikuchita bwino.
"Akhala masewero ovuta poti Karonga ikuchita bwino komabe ife takhonzeka kuti tikachite bwino, anyamata tawauza kuti akapita kutsogolo azigwiritsa ntchito mwayi uliwonse omwe aziupeza." Anatero Sibale.
Iye wati chipambano mtsiku la lero chikhale chabwino kwambiri poti timuyi ichoka kumunsi komwe iwo ali ndikuti asadzatuluke mu ligi ya TNM.
Eagles ili pa nambala yachitatu kuchokera kumunsi pomwe ali ndi mapointsi 20 pa masewero 19 omwe asewera mu ligi ya chaka chino.
"SITINAFIKEPO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake sinafikepo pomwe akuyang'ana zokumana ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Karonga lamulungu.
Kajawa wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati masewero ndi Blue Eagles ndi osiyana ndipo akuyenera kuwatenganso mosiyana komanso osawaderera.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti Eagles ndi timu Ina yabwino, tisawaphweketse chifukwa ali kumunsi koma tikuyenera kuti tiwalemekeze ndikukasewera kuti tipambane"
"Sitikutengera kuti tinawagonjetsa 1-0 pa kwawo kapenaso kuti tikupambana ayi, tisakomedwe ndipo sitinafikepo, tikuyang'anabe masewero aliwonse paokha." Anatero Kajawa.
Karonga ili pa nambala 6 ndi mapointsi 27 pa masewero 20 ndipo sinatayeko mapointsi pansi pa Kajawa.
CHAWANANGWA AONONGA MATIMU
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, wagoletsa chigoli chake chachiwiri mmasewero otsogozana dzulo pomwe timu yake ya Zanaco inagonjetsa Trident FC 2-0 mu ligi ya MTN Supa ligi ku Zambia.
Kaonga anagoletsa chigolichi pa mphindi 34 za masewerowa kuti timuyi itsogole asanabwere Dennis Ndondo pa mphindi 68 za masewerowa kuti timuyi ipeze chipambano chake choyamba mu ligi ya chaka chino.
Chawanangwa tsopano ali ndi zigoli ziwiri mmasewero atatu pomwe anagoletsanso lachitatu ndi FC Muza ndipo timu yake yatolera mapointsi asanu (5) pa masewero atatu tsopano.
#Tawonga2023
Today match
tnm superleageu
OFFICIAL: Tottenham Hotspur has confirmed that Sergio Reguilon has joined Manchester United on loan for the remainder of the 2023/24 season.
OFFICIAL: FC Barcelona and Brighton & Hove Albion Football Club have reached an agreement for the loan of the player Ansu Fati until 30 June 2024. There is no option for a permanent transfer.
He is a good player.
From us all at https://travelguidemalawi.com we wish him good playing season!
MBAMBANDE MANOMA
UEFA EUROPA LEAGUE DRAW
Group A: ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ West Ham ๐ฌ๐ท Olympiacos ๐ฉ๐ช Freiburg ๐ท๐ธ Baฤka Topola
Group B: ๐ณ๐ฑ Ajax ๐ซ๐ท Marseille ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Brighton ๐ฌ๐ท AEK Athens
Group C: ๐ด๓ ง๓ ข๓ ณ๓ ฃ๓ ด๓ ฟ Rangers ๐ช๐ธ Real Betis ๐จ๐ฟ Sparta Praha ๐จ๐พ Limassol
Group D: ๐ฎ๐น Atalanta ๐ต๐น Sporting ๐ฆ๐น Sturm ๐ต๐ฑ Rakรณw
Group E: ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Liverpool ๐ฆ๐น LASK ๐ง๐ช Union SG ๐ซ๐ท Toulouse
Group F: ๐ช๐ธ Villarreal ๐ซ๐ท Rennes ๐ฎ๐ฑ M. Haifa ๐ฌ๐ท Panathinaikos
Group G: ๐ฎ๐น Roma ๐จ๐ฟ Slavia Praha ๐ฒ๐ฉ Sheriff ๐จ๐ญ Servette
Group H: ๐ฉ๐ช Bayer Leverkusen ๐ฆ๐ฟ Qarabaฤ ๐ณ๐ด Molde ๐ธ๐ช BK Hรคcken
๐จ OFFICIAL: Arsenal defender Nuno Tavares has joined Nottingham Forest on a season-long loan.
BREAKING: Chelsea have officially announced the signing of Cole Palmer from Manchester City in a deal worth ยฃ42.5m.
The midfielder signs a seven-year deal with an option for an extra year.
He will wear the number 20 shirt.
BANDA WAPITIRATU KU FLAMES
Katswiri yemwe wabwerera kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Banda, wakalowa mu m'bindikiro wa Flames patangotha maola ochepa atasewera masewero ake oyamba ku Bullets.
Katswiriyu anasewera mphindi 45 za masewero omwe Bullets inachita kuchokera kumbuyo kuti igonjetse Civo United 3-2 ndipo anatenga gawo lalikulu kuthandiza chigoli chachiwiri.
Iye ayamba nawo zokonzekera za timuyi lero pomwe akukonzekera masewero atimu ya Flames ndi Guinea mmasabata awiri akudzawa.
KAONGA WAMWETSA CHOYAMBA CHA CHAKA CHINO
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, wagoletsa chigoli chake choyamba mu ligi ya MTN Super League yaku Zambia pa masewero omwe timu yake yalepherana 1-1 ndi FC Muza lachitatu.
Kaonga anamwetsa pa mphindi 40 mchigawo choyamba kuti ZANACO itsogole komatu Muza inabwenza pa mphindi 52 za masewerowa kudzera pa penate.
Timu ya Zanaco tsopano ili ndi ma points awiri pa masewero awirinso omwe yasewera kamba koti yafananitsa mphamvu mmasewero onsewa.
MHANGO WAYAMBAPO
Katswiri wa Flames, Gabadinho Mhango wagoletsa chigoli chake choyamba kutimu ya Moroka Swallows pomwe timuyi yapha Cape Town Spurs 3-1 mu DSTV Premiership dzulo ku South Africa.
Mhango yemwe anapatsidwa mpata oyamba mmasewerowa anapita mpira kudzera pa free kick kuti apeze chigoli chachitatu cha timuyi mchigawo choyamba.
Iye wafika kumene kutimuyi kuchokera ku Amazulu yomwe inathetsa mgwirizano wake pomwe ligi ya mdzikomo inatsala pang'ono kuyamba.
2023/24 UEFA CHAMPIONS LEAGUE FULL DRAW
Group A ๐ฉ๐ช Bayern ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Man Utd ๐ฉ๐ฐ Copenhagen ๐น๐ท Galatasaray
Group B ๐ช๐ธ Sevilla ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Arsenal ๐ณ๐ฑ PSV ๐ซ๐ท Lens
Group C ๐ฎ๐น Napoli ๐ช๐ธ Real Madrid ๐ต๐น Braga ๐ฉ๐ช Union Berlin
Group D ๐ต๐น Benfica ๐ฎ๐น Inter ๐ฆ๐น FC Salzburg ๐ช๐ธ Real Sociedad
Group E ๐ณ๐ฑ Feyenoord ๐ช๐ธ Atlรฉtico Madrid ๐ฎ๐น Lazio ๐ด๓ ง๓ ข๓ ณ๓ ฃ๓ ด๓ ฟ Celtic
Group F ๐ซ๐ท PSG ๐ฉ๐ช Dortmund ๐ฎ๐น Milan ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Newcastle
Group G ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Man City ๐ฉ๐ช RB Leipzig ๐ท๐ธ Crvena zvezda ๐จ๐ญ Young Boys
Group H ๐ช๐ธ Barcelona ๐ต๐น Porto ๐บ๐ฆ Shakhtar ๐ง๐ช Royal Antwerp
OFFICIAL: Romelu Lukaku has been unveiled as a new AS Roma player.
The Belgian striker joins AS Roma on a loan deal until June 2024.
Silver Strikers
๐๐๐๐ ๐๐ข๐ก๐: Monaco have signed Folarin Balogun from Arsenal for โฌ45M on a contract until June 2028.
"AKANATIPATSA MASEWEROWA KUMAPETO A SABATAYI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wadandaula ndi mmene masewero akuwapezera ponena kuti masewero awo ndi Civo United akanapatsidwa kumapeto kwa sabatayi osati lachitatu kuti osewera apumeko.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake sinapange zokonzekera zokwana komabe akonzeka kukakumana ndi Civo.
"Ndi zoonadi kuti masewero akutipeza pafupifupi, apa tinali ndi masewero mu CAF Champions league kenako lolemba anyamata anapuma pomwe sanapange zokonzekera ndipo lachiwiri anangoziongola nde masewero awa mwina akatipatsa kumapeto kwa sabata ino poti sitinapatsidweko masewero aliwonse." Anatero Munthali.
Iye wati masewerowa akhala ovuta kutengera kuti Civo amavutitsana nawo koma akudziwa kufunikira kopambana masewerowa. Chaka Chatha, pa bwalo pomwepa matimuwa analepherana 1-1 ndipo zinathanso motero mchigawo choyamba.
"UKADAULO WA PETER BANDA UTITHANDIZA MU CAF" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati kubwereranso kwa katswiri wa Flames, Peter Banda, kutimuyi kuwathandiza kuti aonjezere mphamvu mu CAF Champions league ndi zikho za mdziko muno.
Iye amayankhula izi pomwe katswiriyu amasaina mgwirizano wake wa miyezi inayi ndipo Munthali wati akukhulupilira kuti Banda ndi osewera yemwe Bullets idalire kwambiri mmasewerowa akuluakulu.
"Ndi zoona kuti Peter Banda wabwerera ku Bullets atathetsa mgwirizano wake ndi Simba, kubwera kwake kutithandiza makamaka ndi ukadaulo omwe ali nawo omwe watenga ku Simba yomwenso imasewera mu CAF nde arithandizira kwambiri mmasewero ngati amenewa." Anatero Munthali.
Iye wati katswiriyu akuyenera kulimbikira kutengera kuti anyamata ena omwe wawapeza kutimuyi nawo akuchita bwino. Banda wachoka kutimuyi kutsatira kusapeza mpata wosewera pomwe anakumana ndi vuto lovulalavulala.
CIVO YAKONZEKA KUGWETSA BULLETS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake ndi yokonzeka kukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe matimuwa atengerane ku ndewu yamu TNM Supa ligi lachitatu pa bwalo la Kamuzu.
Chidati amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati mkhope zonse mutimuyi zikuoneka zokonzekera masewerowa ndipo wati zomwe akupitira ndi chipambano.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tikukumana ndi timu Ina yabwino komabe mpira umapanga zimene ziliko tsiku limenelo, ife tikayesetsa kuti tikapeze zotsatira zabwino." Anatero Chidati.
Iye wati timuyi ilibe yemwe ali ovulala patsogolo pa masewerowa ndipo wati anyamata akonzeka kwambiri. Civo ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe yatolera mapointsi 24 mmasewero 18.
"MASAMU OTSALIRA MU LIGI NDI OPHWEKA" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Andrew Bunya, wati timu yake ikadali ndi mwayi waukulu otsala mu ligi ya TNM pomwe akuyenera kutolera mapointsi mmasewero omwe atsala nawo kuti asatuluke mu ligi.
Bunya amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Mighty Wakawaka Tigers ndipo iye anati masewerowa amayenera kupambana kuti zinthu zisaipe koma satuluka.
"Tagonja mmasewero ofunikira kwambiri chifukwa tikanawina bwenzi titayandikira chakumtundako koma apapa sikuti kwatha, masamu ake ndi masewero khumi atsalawa ndi mapointsi 30, kuphatikiza 14 ndi 44, mwayi ndi wambiri tingolimbikira." Anatero Bunya.
Timu ya Extreme ili pansi pa ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi 14 pa masewero 20 omwe yasewera ndipo yatsala ndi masewero 10 kuti amalize ligi ya chaka chino.
BANGWE YAKONZEKA KUKUMANA NDI EKWENDENI
Timu ya Bangwe All Stars kudzera mwa mphunzitsi wawo, Abel Mkandawire, yati ndi yokonzeka kukumana ndi timu ya Ekwendeni Hammers pomwe matimuwa akhale akugwebana lachitatu pa bwalo la Rumphi mu ligi ya TNM.
Mkandawire wati timu yake ilibwino ndipo alinso ndi anyamata abwino paliponse omwe akuyembekeza kuwagwiritsa ntchito mmasewero awo ndi Hammers.
"Tikuyang'anira masewero amenewa, takonzekera kwambiri ndipo anyamata onse alibwino, anyamata abwino kwambiri oti tichita kusankha oti akagwire ntchito koma tsopano takhalitsa kuno ndipo bwaloli talizolowera, tikuyembekezera kuchita bwino." Anatero Mkandawire.
Iye wati masewero awo akhala osiyana ndi Moyale Barracks yomwe anakumana nayo sabata yatha pomwe wati inkamenya mpira wogunda kwambiri kusiyana ndi mmene Ekwendeni imasewerera. Mchigawo choyamba, matimuwa analepherana 0-0 pa bwalo la Mpira.
Karonga united squad
silver strikers fc
PETER BANDA WABWERERA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti yasaina katswiri wawo wakale, Peter Banda, kuti atumikirenso kutimuyi.
Izi zadza pomwe iye wathetsa mgwirizano wake ndi timu ya Simba SC ndipo tsopano wapanga chiganizo chotumikiranso timuyi.
Katswiriyu anapita kutimuyi mu 2019 komwe anathandizira timuyi kutenga chikho cha TNM komanso anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba kuposa onse mu ligi.
Izi zinachititsa kuti timu ya Sheriff Tiraspol yaku Georgia imutenge pa ngongole ya miyezi isanu ndi umodzi ndipo atachokako, timu ya Simba inamutenga koma amavutika kamba kuvulala kwambiri.
BURUMUVU
What is the next game for ntaja united
Takulndlani Ku supr league,tione kumenek
Yeye
๐จ ๐ข๐๐๐๐๐๐๐: Jordi Alba has announced his retirement from international football. ๐๐ช๐ธ
๐ 93 selections โฝ๏ธ 10 goals ๐ Euro 2012 ๐ช๐บ ๐ Nations League 2023 ๐ช๐บ
Raphael Varane will miss the game against Arsenal this weekend due to suffering an injury against Nottingham Forest.
TNM2023
KARONGA SIKUFUNA KUTAYA KANTHU PAKHOMO
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake yakonzeka bwino kuti akumane ndi timu ya Moyale Barracks lachitatu pa bwalo la Karonga ndipo wati chimene akuyang'ana ndi chipambano.
Mphunzitsiyu wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati wawauza anyamata ake kufunikira kopeza zipambano pakhomo.
"Anyamata akonzekera bwino ndipo tsopano chifukwa choti tili pakhomo tikuyenera kupambana ndi chipambano chitithandiza kufikabe kumtunda kwa ligiyi. Anyamata ali bwino ndipo ndi mmene akusewerera, lachitatu tichita bwino." Anafotokoza Kajawa.
Chiyitengereni timu ya Karonga, Kajawa watsogolera ku zipambano ziwiri, 4-1 ndi Ekwendeni Hammers komanso 2-1 ndi Kamuzu Barracks koyenda ndipo timuyi ili pa nambala 10 ndi mapointsi 24 pa masewero 19.
"ODWALA TOKHATOKHA TAKUMANA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati masewero awo ndi timu ya Extreme FC masana a lachiwiri akhale ovuta poti matimu onse akufunitsitsa kutsala mu ligi koma ali kunsi kwa ligi.
Nyambose wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati ngakhale kuti zinthu zikuvuta, timu yake ikupita mmasewerowa ndi cholinga chopambana mmasewerowa kuti achoke kumunsi kwa ligi koma watibe wakufa saopa kuola.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse takhalitsa ku mzere ofiira nde tikamakumana chonchi zimavuta komabe ifeyo takhalitsa kumene kuja, tikufunitsitsa titachokako kumene kuja kuti tifikire ku mtundako nde anyamata tawauza kufunikira kopambana masewero amenewa." Anatero Nyambose.
Iye wati masewerowa awatenge ngati a ndime yotsiriza poti sipabweranso ena kudzakumana ndi Extreme. Tigers ikuchokera kogonja 3-1 ndi Blue Eagles ndipo ili pa nambala 13 ndi mapointsi 18.
"CHIPAMBANO CHITITHANDIZA KUCHOKA KUMUNSI" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati masewero awo ndi timu ya Mighty Wakawaka Tigers lachiwiri akhale ofunikira kwambiri pomwe awaonetse tsogolo lowala loti atsalebe mu ligi ya TNM chaka chino.
Kafoteka amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Nankhaka ndipo wati wawauza osewera kuti akaikepo mtima kuti apambane mmasewerowa.
"Ndi masewero ofunikira kutimu yathu mwina kuposa ena aliwonse chifukwa tikapambana tiyandikira matimu atatu ndipo titseka mpata omwe unalipo ndekuti ulendo ofuna kutsala mu ligi ukhale owala. Pali masewero omwe timagonja chifukwa anyamata sanaikirepo mtima koma awa okha tawapempha kuti aikepo mtima." Anatero Kafoteka.
Timu ya Extreme ikuchokera kufanana mphamvu ndi Silver ndipo sikhala ndi Frank Sanudi pokumana ndi Tigers kamba ka zikalata zachikasu zitatu. Iyo ili pansi pa ligi ndi mapointsi 14 pa masewero 19.
IDANA SAPEZEKA NDI GUINEA
Katswiri wa timu ya Flames, Chimwemwe Idana, sapezeka mmasewero omwe timuyi ikumane ndi Guinea pa 10 September kamba koti ali ndi makalata achikasu awiri omwe anawatenga mmasewero ndi Egypt komanso Ethiopia mmiyezi iwiri yapitayo.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi lomwe latsimikiza za nkhaniyi pomwe timuyi yayamba zokonzekera zawo lolemba ndipo Idana anali konko.
Katswiriyu wapita kutimuyi ngati opanda timu pomwe zomwe amafuna kuti apite ku Zambia zikuvuta ndipo tsopano ali ndi mwayi osewerera Mbeya City yokha yomwe inatuluka mu ligi yaikulu ku Tanzania.
TEMWA AKUTSOGOLA ZIGOLI, TABITHA AKUGOLETSANSO
Akatswiri a timu ya Scorchers, Temwa Chawinga ndi Tabitha Chawinga, akuchita bwino kutimu yawo ya Wuhan Jiangda ku China pomwe lamulungu agoletsa zigoli zitatu aliyense pomwe timu yawo yapha Guangdong Meizhou 8-1 mu ligi ya China Women's Football.
Temwa tsopano wafika pa zigoli 18 pa masewero 14 omwe wasewera kutimuyi ndipo akutsogola mu ndandanda wa osewera omwe akugoletsa zigoli zambiri ndipo Barbra Banda waku Zambia akutsatira ndi zigoli 11.
Naye Tabitha wamwetsa zigoli zisanu (5) mu ligiyi pa masewero atatu omwe wasewera chichokereni ku Inter Milan yaku Italy. Wuhan ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi 40, asanu pamwamba pa timu ya Shanghai RCB pa masewero 14 omwe asewera.
Temwa watengapo kale mphoto zokhala katswiri womwetsa zigoli zambiri zikho ziwiri kale chaka chino ndipo ngati apambane mphotoyi, ikhale yachitatu mu chaka chokha chino.
BANDA WASIYANA NDI SIMBA
Katswiri wa timu ya Flames, Peter Banda, tsopano ali ndi ufulu wopita ku timu iliyonse pomwe timu ya Simba SC yalengeza kuti yasiyana ndi katswiriyu.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lolemba pomwe timuyi yathokoza katswiriyu kamba kokhala ndi timuyi mu zaka ziwiri kutsatira kumusaina kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets mu 2021.
Banda wavutika kuti akhazikike kutimuyi pomwe amangovulala nthawi zambiri kupangitsa kuti asewera masewero ochepa ngakhale kuti amakondedwa kutimuyi.
Zamveka kuti osewerayu akhonza kubwereranso ku Bullets pomwe akufuna kuzitolera kuti azigulitsenso kunja kwa dziko lino.
"TIMUSOWA FODYA MMASEWERO ENAWA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timuyi imusowa katswiri wawo, Yamikani Fodya, yemwe sapezeka mmasewero awo a ndime Ina yomwe akumane ndi TP Mazembe mu CAF Champions league kamba koti anapatsidwa kalata yofiira dzulo mmasewero awo ndi Dragon.
Katswiriyu analandira chikalatachi anaponda osewera wa Dragon komabe timuyi inapambana masewerowa 1-0 kuti afike mu ndime yachiwiri yachipulula ya chikhochi 3-0 pa zigoli zonse. Munthali anati timu yawo inataya mipata kwambiri ndipo azikonza mmasewero akubwerawa.
Iye anatinso Fodya wakhala ofunikira kwambiri kutimuyi komabe kusapezeka kwake kuwapangitsa kuti ena awagwiritse ntchito mmasewero akudzawa.
"Zoonadi Fodya wakhala wofunikira masewero athu makamaka ndi ukadaulo omwe ali nawo ndipo kusapezeka kwake timusowa koma tili ndi anyamata ena omwe tiwakodole kuti agwire ntchito, tinali nawo ena anavulala ndipo apa agwira ntchito." Anatero Munthali.
Bulle
"WE ARE TOP WE NEED TO STAY THERE" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says he is happy with his team's win against MAFCO that took them top of the table and highlighted the importance of staying there despite facing a four-teams race to the championship.
Harrison said this after a 1-0 win over the soldiers, thanks to a Gaddie Chirwa's 53rd minute goal and the coach said the game was very tough but lucky that they got the win.
"It was a very difficult game you know, we wasted two good chances in the second half that could put us to three or four games but in the first half we were not playing we were very low but second half we improved and showed agency, it was tough but good that we have won." Said Harrison.
The Briton further said it is good that the team is top and have to develop a winning mentality to remain at the position but a the competition for the Championship is very hard in the league. The Nomads are now top after having 36 points from 19 ga
"TITHOKOZE OYIMBIRA AWATHANDIZA A WANDERERS" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu ya Wanderers yawagonjetsa lamulungu chifukwa cha thandizo la oyimbira yemwe ziganizo zake zinakondera timuyi.
Mwansa amayankhula izi atatha masewero ndi timuyi ndipo Wanderers inapambana 1-0 ndi chigoli cha Gaddie Chirwa. Iye wati ndi zoonadi kuti matimu ena akumathandizidwa ndi oyimbira.
"Tithokoze oyimbira kuti wathandiza timu ya Wanderers kuti ipambane chifukwa ziganizo zonse zimakomera anzathuwa, ndivomereze kuti oyimbira ena akumasankhadi matimu oti awathandize nde lero zimene amafuna zachitika, kugwira mu box osayimba ayi." Anatero Mwansa.
Mmasewerowa, katswiri wa MAFCO, Ernest Tambe, anaonetsedwa chikalata chofiira ndipo osewera okwana asanu ndi awiri analandira makalata achikasu. Kutsatira kugonjaku, MAFCO ili pa nambala 14 ndi mapointsi 18 pa masewero 19.
"INALI PENATE YENIYENI, OSEWERAWA AZIGANIZA" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wapempha osewera atimu yake kuti akamasewera mpira aziganiza osati kuchita chibwana ngati akufuna kuti azichita bwino mu ligi.
Mhango wayankhula izi atatha masewero awo ndi Bangwe All Stars omwe analepherana 1-1 ndi chigoli cha penate cha Kondwani Chilembwe nthawi yotha itha chinakaniza chigoli cha Gastin Simkonda kuti chipezetse chipambano timuyi.
Mhango anati timu yake inavutika ndi bwalo la tsopano komanso kaseweredwe koponda ka Bangwe koma chibwana chawapweteka.
"Masewero anali abwino, tinavutika pa malo atsopano komabe tinasewera tinapeza chigoli koma mchigawo chachiwiri anzathuwa anabwera moponda zomwe zinativuta, anapeza penate yabwinobwino ndipo agoletsa tafanana mphamvu." Iye anatero.
Iye wati osewera akufunika aziyikapo mtima ngati akufuna azipambana pomwe timuyi tsopano ili pa nambala 11 ndi mapointsi 23 mu ligi ya TNM.
KAMWENDO WAKHUTIRA NDI POINT IMODZI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati ndi okhutira ndi kufanana mphamvu kwa timuyi ndi Moyale Barracks koyenda pamene wati pointi yomwe atengayo yawathandiza kusunthira kumtunda kwa ligi.
Kamwendo amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Rumphi pomwe matimuwa analepherana 1-1 ndi zigoli za Gastin Simkonda komanso Kondwani Chilembwe. Iye anayamikira timu yake kuti inasewera bwino.
"Tasewera bwino kwambiri mwina mchigawo choyamba timavutikirabe pang'ono koma ndasangalala ndi mphamvu zomwe osewera anaika mchigawo chachiwiri mpaka tapeza chigoli, kuphonya ndi ntchito yathu kuti tiwakonze koma achita bwino ndithu." Anatero Kamwendo.
Timuyi tsopano ili pa nambala 6 mu ligi ndi mapointsi 25 pa masewero 19 ndipo akusewera masewero awo otsatira lachitatu pomwe akumane ndi Ekwendeni Hammers pa bwalo la Rumphi lomweli.
"TIKUONONGA NDALAMA POMWE OYIMBIRA AKUONONGABE ZINTHU" - MAPASULA
Mmodzi mwa akuluakulu ophunzitsa timu ya Red Lions, Chifundo Mapasula, wadandaula ndi oyimbira yemwe anali pa masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos ponena kuti watengapo mbali kuti timu yake igonje mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero awo omwe agonja 2-0 ndi timu ya Dedza Dynamos ndipo wati mchitidwe wa oyimbira ukusokoneza matimu ambiri mdziko muno.
"Oyimbira watengapo mbali sinali penate, osewera uja mpira unamumenya pa phewa koma apereka penate zomwe zikuchitikazi akutipondereza kwambiri chifukwa tikugwiritsa ntchito ndalama tikamasewera mpirawu koma oyimbira akumakhala ndi matimu nde nzosokoneza." Anatero Mapasula.
Iye anati timuyi inalinso ndi mavuto ena ochepa omwe akonze patsogolo pa masewero awo otsatira. Lions ili pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18.
CHIRWA WADERA NKHAWA NDI KUVULALA KWA NYONDO NDI CHIPALA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati akukhulupilira kuti osewera ake omwetsa zigoli awiri atimu yake, Clement Nyondo ndi Charles Chipala, apezeka mmasewero otsatira atimuyi pomwe akatswiriwa avulala mmasewero atimuyi ndi Red Lions lamulungu.
Osewerawa anachita kutulutsidwa pa machira nthawi yakumapeto atavulala mmasewero omwe timu yawo yapambana 2-0 ndipo Nyondo anamwetsa chigoli chachiwiri pomwe Chipala ndi yemwe anasewera bwino kuposa onse.
Koma Chirwa wati ali ndi chikhulupiliro kuti anyamatawa apezekabe kutimuyi kutengera kufunikira kwawo kutimuyi.
"Ndi anyamata ofunikira kwambiri ndi omwe atithandiza mmasewero ambiri nde ndikukhulupilira kuti tikhalabe nawo ndipo tingowafunira zabwino zonse.
Timu ya Dedza ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe yatolera mapointsi 25 pa masewero 19 omwe yasewera ndipo Nyondo akutsogola pomwe ali ndi zigoli 13 mu ligi ya TNM.
League ya chaka chino sizocheza yatentha!