CHAWANANGWA AONONGA MATIMU
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, wagoletsa chigoli chake chachiwiri mmasewero otsogozana dzulo pomwe timu yake ya Zanaco inagonjetsa Trident FC 2-0 mu ligi ya MTN Supa ligi ku Zambia.
Kaonga anagoletsa chigolichi pa mphindi 34 za masewerowa kuti timuyi itsogole asanabwere Dennis Ndondo pa mphindi 68 za masewerowa kuti timuyi ipeze chipambano chake choyamba mu ligi ya chaka chino.
Chawanangwa tsopano ali ndi zigoli ziwiri mmasewero atatu pomwe anagoletsanso lachitatu ndi FC Muza ndipo timu yake yatolera mapointsi asanu (5) pa masewero atatu tsopano.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores