"INALI PENATE YENIYENI, OSEWERAWA AZIGANIZA" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wapempha osewera atimu yake kuti akamasewera mpira aziganiza osati kuchita chibwana ngati akufuna kuti azichita bwino mu ligi.
Mhango wayankhula izi atatha masewero awo ndi Bangwe All Stars omwe analepherana 1-1 ndi chigoli cha penate cha Kondwani Chilembwe nthawi yotha itha chinakaniza chigoli cha Gastin Simkonda kuti chipezetse chipambano timuyi.
Mhango anati timu yake inavutika ndi bwalo la tsopano komanso kaseweredwe koponda ka Bangwe koma chibwana chawapweteka.
"Masewero anali abwino, tinavutika pa malo atsopano komabe tinasewera tinapeza chigoli koma mchigawo chachiwiri anzathuwa anabwera moponda zomwe zinativuta, anapeza penate yabwinobwino ndipo agoletsa tafanana mphamvu." Iye anatero.
Iye wati osewera akufunika aziyikapo mtima ngati akufuna azipambana pomwe timuyi tsopano ili pa nambala 11 ndi mapointsi 23 mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores