TEMWA AKUTSOGOLA ZIGOLI, TABITHA AKUGOLETSANSO
Akatswiri a timu ya Scorchers, Temwa Chawinga ndi Tabitha Chawinga, akuchita bwino kutimu yawo ya Wuhan Jiangda ku China pomwe lamulungu agoletsa zigoli zitatu aliyense pomwe timu yawo yapha Guangdong Meizhou 8-1 mu ligi ya China Women's Football.
Temwa tsopano wafika pa zigoli 18 pa masewero 14 omwe wasewera kutimuyi ndipo akutsogola mu ndandanda wa osewera omwe akugoletsa zigoli zambiri ndipo Barbra Banda waku Zambia akutsatira ndi zigoli 11.
Naye Tabitha wamwetsa zigoli zisanu (5) mu ligiyi pa masewero atatu omwe wasewera chichokereni ku Inter Milan yaku Italy. Wuhan ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi 40, asanu pamwamba pa timu ya Shanghai RCB pa masewero 14 omwe asewera.
Temwa watengapo kale mphoto zokhala katswiri womwetsa zigoli zambiri zikho ziwiri kale chaka chino ndipo ngati apambane mphotoyi, ikhale yachitatu mu chaka chokha chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores