CHIRWA WADERA NKHAWA NDI KUVULALA KWA NYONDO NDI CHIPALA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati akukhulupilira kuti osewera ake omwetsa zigoli awiri atimu yake, Clement Nyondo ndi Charles Chipala, apezeka mmasewero otsatira atimuyi pomwe akatswiriwa avulala mmasewero atimuyi ndi Red Lions lamulungu.
Osewerawa anachita kutulutsidwa pa machira nthawi yakumapeto atavulala mmasewero omwe timu yawo yapambana 2-0 ndipo Nyondo anamwetsa chigoli chachiwiri pomwe Chipala ndi yemwe anasewera bwino kuposa onse.
Koma Chirwa wati ali ndi chikhulupiliro kuti anyamatawa apezekabe kutimuyi kutengera kufunikira kwawo kutimuyi.
"Ndi anyamata ofunikira kwambiri ndi omwe atithandiza mmasewero ambiri nde ndikukhulupilira kuti tikhalabe nawo ndipo tingowafunira zabwino zonse.
Timu ya Dedza ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe yatolera mapointsi 25 pa masewero 19 omwe yasewera ndipo Nyondo akutsogola pomwe ali ndi zigoli 13 mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores