"TITHOKOZE OYIMBIRA AWATHANDIZA A WANDERERS" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati timu ya Wanderers yawagonjetsa lamulungu chifukwa cha thandizo la oyimbira yemwe ziganizo zake zinakondera timuyi.
Mwansa amayankhula izi atatha masewero ndi timuyi ndipo Wanderers inapambana 1-0 ndi chigoli cha Gaddie Chirwa. Iye wati ndi zoonadi kuti matimu ena akumathandizidwa ndi oyimbira.
"Tithokoze oyimbira kuti wathandiza timu ya Wanderers kuti ipambane chifukwa ziganizo zonse zimakomera anzathuwa, ndivomereze kuti oyimbira ena akumasankhadi matimu oti awathandize nde lero zimene amafuna zachitika, kugwira mu box osayimba ayi." Anatero Mwansa.
Mmasewerowa, katswiri wa MAFCO, Ernest Tambe, anaonetsedwa chikalata chofiira ndipo osewera okwana asanu ndi awiri analandira makalata achikasu. Kutsatira kugonjaku, MAFCO ili pa nambala 14 ndi mapointsi 18 pa masewero 19.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores