BANGWE YAKONZEKA KUKUMANA NDI EKWENDENI
Timu ya Bangwe All Stars kudzera mwa mphunzitsi wawo, Abel Mkandawire, yati ndi yokonzeka kukumana ndi timu ya Ekwendeni Hammers pomwe matimuwa akhale akugwebana lachitatu pa bwalo la Rumphi mu ligi ya TNM.
Mkandawire wati timu yake ilibwino ndipo alinso ndi anyamata abwino paliponse omwe akuyembekeza kuwagwiritsa ntchito mmasewero awo ndi Hammers.
"Tikuyang'anira masewero amenewa, takonzekera kwambiri ndipo anyamata onse alibwino, anyamata abwino kwambiri oti tichita kusankha oti akagwire ntchito koma tsopano takhalitsa kuno ndipo bwaloli talizolowera, tikuyembekezera kuchita bwino." Anatero Mkandawire.
Iye wati masewero awo akhala osiyana ndi Moyale Barracks yomwe anakumana nayo sabata yatha pomwe wati inkamenya mpira wogunda kwambiri kusiyana ndi mmene Ekwendeni imasewerera. Mchigawo choyamba, matimuwa analepherana 0-0 pa bwalo la Mpira.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores