Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
𝗕𝗥𝗘𝗔𝗞𝗜𝗡𝗚‼️
Germany have sacked Hansi Flick after their embarrassing 4-1 defeat to Japan.
🚨 Hansi Flick's Germany's Last 5 International Games! 🇩🇪⬇️
❌🇧🇪 Belgium 3-2 Germany 🇩🇪 🤝 🇩🇪 Germany 3-3 Ukraine 🇺🇦 ❌ 🇵🇱 Poland 1-0 Germany 🇩🇪 ❌ 🇩🇪 Germany 0-2 Colombia 🇨🇴 ❌ 🇩🇪 Germany 1-4 Japan 🇯🇵
‣ Finished 3rd in The UNL 2022-23 Group Stage Behind Italy & Hungary ❌
TEMWA CHAWINGA WAFIKITSA ZIGOLI 22
Katswiri watimu ya Scorchers, Temwa Chawinga, wakwanitsa zigoli 22 mu ligi ya mdziko la China ya amayi pomwe lachisanu anagoletsa zigoli zitatu kuti Wuhan Jiangda igonjetse Beijing Beikong 8-0 mu ligiyi.
Chawinga akutsogola ndi zigoli mu ligiyi pomwe chipambanochi chathandiziranso Wuhan kutsogola ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero 16 omwe asewera ndipo ali ndi mapointsi 46.
Ligi ya mdzikomo yaima kaye ndipo idzayambanso pa 4 November kuti matimu adzamalizitse masewero omwe atsalawo. Temwa wapambana kale mphoto zogoletsa zigoli zambiri mdzikoli ziwiri mu chaka chokha chino.
#Tawonga2023
MUNTHALI NDI CHAWANANGWA SAPEZEKA KWA MASABATA ATATU
Osewera awiri atimu ya Flames omwe amasewera kunja kwa dziko lino, Chawanangwa Kaonga ndi Brighton Munthali akhala masabata atatu asakugunda mpira kamba koti anavulala mmasewero omwe timuyi yalepherana 2-2 ndi Guinea loweruka pa bwalo la Bingu.
Munthali anavulala mchigawo choyamba ndipo anasinthana ndi Clever Nkungula pomwe Chawanangwa anavulala mu nthawi yoonjezera atagundana ndi osewera a Guinea.
Osewera onsewa athandizidwa ndipo auzidwa kuti asasewere kwa masabata atatu ndipo akaunikidwanso akapita ku matimu awo. Chawanangwa amasewera timu ya ZANACO ku Zambia pomwe Munthali ndi goloboyi wa Black Leopards yaku South Africa.
Kd karonga yiwina
PAIPI WALOWA MMANDA
Thupi la Katswiri wakale wa timu ya Silver Strikers, Thuso Paipi, lalowa mmanda loweruka masana ku manda a HHI ku Blantyre.
Katswiriyu anamwalira lachisanu pa chipatala cha Queen Elizabeth komwe anamugoneka kwa masiku awiri atadwala.
Anthu ochuluka anapita ku mandaku kukapereka ulemu omaliza kwa katswiriyu yemwe anapambana chikho cha Airtel Top 8 choyamba mu 2017 ndi Silver Strikers.
Tidzaonananso mmoyo winawo.
SAIZI NDI CHAZIYA AMWETSA ZIGOLI ZOYAMBA KU FLAMES
Osewera atimu ya Flames, Robert Saizi komanso Lawrence Chaziya, atsegula matumba awo azigoli kutimuyi pomwe anamwetsa chigoli chimodzi aliyense kuti Flames ilepherane 2-2 ndi Guinea pa bwalo la Bingu loweruka masana.
Saizi anamwetsa chigoli chake choyamba ndi timuyi pa mphindi 23 anamalizitsa mpira omwe Lanjesi Nkhoma anamenyetsa munthu mu masewero ake achisanu ndi timuyi. Malawi inagoletsetsa zigoli ziwiri mu mphindi zitatu pomwe Aguibou Camara komanso Saidou Sow anamwetsa zigoli pa mphindi 56 ndi 58 aliyense kuti Guinea itsogole 2-1.
Masewero akupita kumapeto, Saizi anamenya Kona yomwe Chaziya anasumbira mu ukonde kuti apezenso Chigoli chake choyamba ndi timuyi mmasewero ake achikhumi chomwe chaletsa Flames kugonja.
Mu gulu la timuyi, Flames yathera pachitatu ndi mapointsi asanu pa masewero asanu ndi amodzi ndipo Egypt ndi Guinea ndi omwe achoka mu gululi ndikupita ku mpikisano wa African Cup of Nations wa 2023.
malawi tiyeni tilimbikikle
BANDA WAYAMIKIRA OSEWERA ACHISODZERA KU FLAMES
Mtsogoleri wa osewera kutimu ya Flames, John Banda, wayamikira osewera omwe ndi achisodzera kutimuyi kamba kochita bwino ndi timuyi ku mpikisano wa COSAFA komwe anathera pa nambala yachinayi.
Banda amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Guinea yomwe iye walonjeza kuti iwo apanga kuthekera kulikonse kuti apambane.
Iye wati osewera achisodzera akuchita bwino kwambiri kutimuyi ndipo ngati angagwirane manja ndi achiyambakale akutimuyi, timuyi ipambana masewerowa.
Malawi ikukumana ndi Guinea mu masewero opitira ku mpikisano wa African Cup of Nations koma matimu omwe anadutsa kale ndi Egypt komanso Guinea yomweyi.
ANYAMATA ANAYI ACHIRA, ATATU AKADALI OVULALA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets itha kukhala yokondwa kwambiri kamba koti idzakhala ndi anyamata ake anayi, Hassan Kajoke, Patrick Mwaungulu, Eric Kaonga ndi Precious Sambani mmasewero awo ndi TP Mazembe mu CAF Champions league poti iwo achira.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Heston Munthali, ndi yemwe wanena izi pomwe amayankhula ndi olemba nkhani akutimuyi pa nkhani mmene osewera alili.
Iye wati Mwaungulu, Kajoke ndi Kaonga apanga zokonzekera zonse ndi timuyi sabata yonse ndipo Sambani ayamba lolemba pomwe wati ali tsopano bwino. Osewera atatu, Stanley Biliati, Alick Lungu ndi Mike Mkwate sapezeka mmasewerowa.
Mkwate sapezeka kwa ligi ya chaka chino yonse pomwe Biliati ndi Lungu ayambapo mmasabata atatu akudzawa. Bullets ikumana ndi Mazembe lamulungu lapa 17 September pa bwalo la Bingu asanakakumanenso pakhomo pa Mazembe ku DRC.
THUSO PAIPI WAMWALIRA
Katswiri wakale wa timu ya Sure stream Academy komanso Silver Strikers, Thuso Paipi, wamwalira.
Malume ake a katswiriyu ndi omwe atsimikiza kuti katswiriyu watisiya atadwala kwa masiku awiri omwe anamugoneka ku chipatala cha Queen Elizabeth ku Blantyre lachisanu.
Katswiriyu wakhala asakuoneka chichokereni ku timu ya Silver Strikers mu 2020 ndipo watengako nawo chikho cha Airtel Top 8 mu 2017 ndi Silver.
Very sad! 😢 MHSRIP
🚨 𝐁𝐑𝐄𝐀𝐊𝐈𝐍𝐆: Liverpool captain Virgil van Dijk has been given a further one-match ban and fined £100,000.
Van Dijk will miss next weekend's trip to Wolves after admitting that he acted in an improper manner and used abusive and insulting words towards a match official.
KUSINTHA KUKUONEKA KU EAGLES
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati timu yake yayamba kuonetsa kusintha pomwe ayamba kutolera mapointsi mmasewero omwe asewera posachedwa.
Eagles inagonjetsa Mighty Wakawaka Tigers ndipo yafanana mphamvu mmasewero awo sabata yatha ndipo patsogolo pa masewero awo ndi Civo United pa bwalo la Champions ku Dowa, Sibale wati akonzeka.
"Tinafika mu Lilongwe ndipo tayamba kukonzekera masewero ndi Civo, zikuoneka kuti zinthu zayamba kuyenda ndipo zitati zipitilire ndekuti tikhonza kuchoka kumunsi kumene tili kuja." Anatero Sibale.
Timu ya Blue Eagles ikadali ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe ili pa nambala 14 ndi mapointsi 21 pa masewero 20.
2-4
BULLETS NDI WANDERERS ALI PAKHOMO MU FDH BANK CUP
Matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets akhala pakhomo mmasewero awo amu chikho cha FDH Bank pomwe bungwe la Football Association of Malawi laika masewero amu ndime yamatimu onse pa bwalo la Kamuzu.
Bungweli latulutsa ndandanda wa masewerowa omwe akuonetsa masiku komanso malo omwe adzasewerere masewerowa.
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers idzakumana ndi MAFCO pa bwalo la Kamuzu loweruka la pa 16 September komwe FCB Nyasa Big Bullets idzalandira timu ya Dedza Dynamos pa bwalo lomweli lamulungu pa 24 September. Umu ndi mmene masewero onse akhalire mu chikhochi.
LOWERUKA, 16 SEPTEMBER 2023
•Mighty Mukuru Wanderers vs MAFCO @ Kamuzu Stadium
LAMULUNGU, 24 SEPTEMBER 2023
•FCB Nyasa Big Bullets vs Dedza Dynamos @ Kamuzu Stadium
Wolemba ndi Hastings Wadza Kasonga Jr
Part-cee sapotazi wa manoma.
"MWINA MATIMU TIZINGOSONKHERANA NKUMAIMBIRA TOKHA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Oscar Kaunda, wadandaula kuti oyimbira wawaonongera masewero pomwe timuyi yagonja 2-0 ndi timu ya MAFCO ku bwalo la Chitowe lachitatu.
Kaunda anayankhula izi masewerowa atatha ndipo wati zigoli zimene Stain Malata anagoletsa zinali zowapatsa ndipo anasewera ndi phuma kuti abwenze zigolizo mpake anakanika kugoletsa mipata yomwe anaipeza.
"Tasewera bwino kwambiri koma mwina mipata sitinathe kuipanga zigoli, komanso mwina bola tizingosonkherana matimu nkumaimbira tokha kuti mwina oyimbirayo aziopa Civo ndi MAFCO chifukwa leroli ationongera masewero mu kanthawi kochepa." Anatero Kaunda.
Iye wati timu yake isewetsa kuti izitolere changu ndi cholinga choti masewero awo a lamulungu adzapambane ndi Blue Eagles. Civo ili pa nambala 11 ndi mapointsi 24.
MKANDAWIRE WATAYIRA KAMTENGO CHIKOOKA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake yagonja mmasewero awo ndi timu ya Chitipa United chifukwa choti goloboyi wa Chitipa United, George Chikooka, anali bwino kwambiri.
Mphunzitsiyu amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Mpira ndipo wati timu imene imataya mimwayi yochuluka imavutika kuti ipeze zigoli mpake yagonja.
"Tinapeza mipata yochuluka koma takanika kupeza zigoli nde timu imene imakanika kugoletsa zimavuta kupambana, anzathuwa anangopeza mipata iwiri agwiritsa ntchito. Leroli George Chikooka anadzuka bwino, timuyamikire ndithu wagwira ntchito yapamwamba." Anatero Mkandawire.
Iye wati timu yake ichilimikabe kuti ipeze zipambano mmasewero akutsatirawa kuti amalize pabwino mu ligi. Bangwe ikadali panambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapointsi 28 pamasewero 21.
"CHIPAMBANO CHINALI CHOFUNIKIRA KWA IFE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati chipambano cha timuyi chinali chofunikira kwambiri kuti aziyendabe bwino kugonjetsa timu ya Civo United 2-0 pa bwalo la Chitowe lachitatu lathali.
Stain Malata anamwetsa zigoli ziwiri mmasewerowa zomwe zathandiza timuyi kupambana ndipo Mwansa wati Civo inasewera mpira wapamwamba koma zigoli za changu zawathandiza kuti apambane.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa Civo yamenya bwino kwambiri komabe anyamata anayesetsa kutsekatseka monse kuti isadutse ndipo zigoli za changu zatithandiza kwambiri, timafunikira kuti tiwine ndithu kuti chitsogolo chikhale chowala." Anatero Mwansa.
Kutsatira kupambanaku, timu ya MAFCO yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 24 pa masewero 21 omwe yasewera. Masewero awo otsatira aliko lamulungu likudzali pa bwalo lomweli ndi Dedza Dynamos.
NGINDE SAKUKONDWA KUKHALA PAMWAMBA PA LIGI
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati sichinthu chokondweretsa kwambiri kuti timu yake tsopano ili pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM pomwe wati cholinga chachikulu ndi choipanga timu kukhala yamphamvu.
Mphunzitsiyu amayankhula izi timu yake itapambana 2-0 ndi Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira ndi zigoli za kumapeto za Ghedo Lorenzo ndi Godfrey Kwiyokwa. Iye wati timu yake simadalira osewera mmodzi mpake atasintha timuyi inayamba kusewera bwino ndipo sakukondwa kwambiri pokhala pamtunda.
"Kwa ineyo sikuti ndine okondwa chifukwa cholinga chimene ndinapitira ku Chitipa ndi chokuti ndiyipange timu ija ikhale yamphamvu mu zaka ziwiri zikubwerazi nde kukhala pa nambala 1, aziyankhula ndi mapointsi osati nambala." Anatero Mtetemera.
Chipambanochi chinali chachiwiri koyenda ndipo chawafikitsa pa nambala yoyamba ndi mapointsi 39 pamwamba pa FCB Nyasa Big Bullets yomwe ikutsalira ndi masewero atatu.
2_0
𝐆𝐮𝐞𝐬𝐬 𝐁𝐚𝐥𝐥𝐨𝐧 𝐝’𝐎𝐫 𝐓𝐎𝐏 𝟑! 🏆✨
Official list of 30 candidates has been now released by France Football for Ballon d’Or ⤵️🏅
Karim Benzema 🇫🇷 Joško Gvardiol 🇭🇷 Jamal Musiala 🇩🇪 André Onana 🇨🇲 Mo Salah 🇪🇬
Randal Kolo Muani 🇫🇷 Jude Bellingham 🏴 Kevin de Bruyne 🇧🇪 Bernardo Silva 🇵🇹 Bukayo Saka 🏴
Khvicha Kvaratskhelia 🇬🇪 Emiliano Martínez 🇦🇷 Erling Haaland 🇳🇴 Nicoló Barella 🇮🇹 Rubén Dias 🇵🇹
Martin Ødegaard 🇳🇴 Ilkay Gündogan 🇩🇪 Julián Álvarez 🇦🇷 Yassine Bono 🇲🇦 Vinicius Jr 🇧🇷
Robert Lewandowski 🇵🇱 Antoine Griezmann 🇫🇷 Lautaro Martínez 🇦🇷 Lionel Messi 🇦🇷 Rodri 🇪🇸
Victor Osimhen 🇳🇬 Kylian Mbappé 🇫🇷 Kim Min-jae 🇰🇷 Luka Modrić 🇭🇷 Harry Kane 🏴
"ATITULUTSA NDI IWOWO KOMA SITINATULUKE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati anthu omwe akuti timuyi yatuluka kale mu ligi ya TNM akuyankhulira mmaganizo awo koma timuyi ikhalabe mu ligiyi.
Mwansa amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe timu yawo ikumane ndi Civo United pa bwalo la Chitowe ndipo wati timuyi ikuyenera kupeza chipambano mwa njira ina iliyonse.
"Akhala masewero ovuta kwambiri koma tikuyenera kuti tichite bwino chifukwa choti sitili pabwino, tili kumunsi nde chipambano chitithandiza kuti tifike kumtundaku. Ife mu ligi sitinatuluke, awo akuyankhulawo ndi maganizo awo koma adzayankhule ligi ikadzatha." Watero Mwansa.
Timuyi ili pa nambala 14 mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero 20 omwe yasewera. Akapambana, timuyi ifike pa nambala 12 ndi mapointsi 24.
"ANGAKHALE OMWE ALI PAMTUNDA SALI SAFE" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo, Wilson Chidati, wati ligi ya chaka chino ikuvuta kwambiri ndipo palibe timu imene ili pa mtendere mu ligi ya TNM ya chaka chino.
Chidati wayankhula izi patsogolo pa masewero a timuyi ndi MAFCO omwe aseweredwe pa bwalo la Chitowe ndipo wati timu yake ikuyenera kupambana kuti ikulitse mwayi womaliza bwino mu ligiyi.
"Akhala masewero ovuta kwambiri chifukwa ligi ya chaka chino akuvuta kwambiri ndipo palibe timu imene ili safe nde ukumati ukapeza point iliyonse, ikumakhala yofunikira kwambiri mu ligiyi. Takonzekera bwino lomwe kuti tikathe kupeza chipambano." Anatero Chidati.
Timu ya Civo ili pa nambala 10 mu ligi ya TNM pomwe ali ndi mapointsi 24 ndipo akapambana afikabe pa mapointsi 27.
BANGWE MISS TWO STARS AGAINST CHITIPHA
Bangwe All Stars will not have their two talented stars, Yamikani Mologeni and Robert Saizi as the two are with Flames when they are facing Chitipa United on Wednesday afternoon.
The team's coach, Abel Mkandawire, confirmed about the news ahead of their match but said this does not deny them a chance to win the match.
"It's going to be a tough match as Chitipa United is also a good side but we are playing at home, getting maximum points today will put us on 31 points which will be good for us. We will not have Mologeni and Saizi who are with Flames but we will have others who will fit into their places." Said Mkandawire.
This is a second meeting between the two sides this season as Chitipa United won 2-1 at the Karonga Stadium in the first round. A win for Bangwe will place them two steps behind the top four.
BULLETS YALEMBETSA PETER BANDA MU CAF
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yamulembetsa katswiri wawo, Peter Banda, pa osewera omwe akutumikira timuyi mu mpikisano wa CAF Champions league.
Mkulu oyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati kupezeka kwa katswiriyu mmasewerowa kudzathandizira kupha mwa nkhanza timu ya TP Mazembe yomwe akumane nayo kawiri mmwezi uno.
Katswiriyu anabwereranso ku Bullets kumapeto a mwezi watha kutsatira kuthetsa mgwirizano wake ndi timu ya SC Simba yaku Tanzania ndipo wasewera masewero amodzi kale ku Bullets omwe inapha Civo United 3-2.
NGINDE WATI CHITIPA SINATOPE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati timu yake sikuti yatopa koma masewero akoyenda amakhala ovuta kwambiri kwa matimu osiyanasiyana.
Nginde wayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Bangwe All Stars pomwe wati timu yake yakonzekera bwino masewerowa ndipo ikuyang'ana za chipambano mtsiku la lero.
"Anyamata akonzekera za kugonja ndi Tigers aziyiwala awa ndi masewero ena omwe tikuyenera kuikapo mtima kuti tipambane. Sikuti anyamata atopa ayi, komano tikayenda mwina zimavuta kuti tipeze zipambano nde koma tikulimbikirabe kuti tizichita bwino." Anatero Mtetemera.
Timuyi ikapambana masewerowa itsogolera ndandanda wa matimu 16 mu ligi ya TNM koma ikhala kuti yasewera masewero ochuluka kusiyana ndi omwe akupikisana nawo. Chitipa ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi 36.
KONDOWE ALIMBIRANA PA MPHOTO YAKU BULLETS
Katswiri watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, apikisana nawo pa mphoto ya osewera omwe asewera bwino mu mwezi wa August angakhale kuti sanayambeko masewero mu TNM Supa ligi.
Kondowe wakhala ofunikira kwambiri ku timuyi mu mweziwu pomwe anagoletsa zigoli zofunikira kwambiri zimene zapulumutsa timuyi kuti isagonje kapenanso kuipambanitsa.
Iye anamwetsa chigoli chofunikira kuti Bullets igonjetse Extreme FC mu FDH Bank ndipo anagoletsanso ndi Mighty Wakawaka Tigers kuti matimuwa afanane mphamvu 1-1, chigoli chogonjetsera Dragon FC mu CAF Champions league komanso chigoli chachiwiri pomwe Bullets inagonjetsa Civo United 3-2.
Enanso omwe apikisane pa mphotoyi ndi katswiri wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa ndi wapakati, Chawanangwa Gumbo.
"TILI PAKHOMO TIKUYENERA KUPAMBANA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati masewero atimu yake akhale ovuta masana a tsiku la lero pomwe akukumana ndi Chitipa United koma wati apanga zothekera kuti apambane.
Mkandawire wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Mpira ndipo wati timu yake ikuyenera kugwiritsa ntchito mwayi wa pakhomo.
"Awa ndi masewero enanso ovuta pomwe Chitipa ndi timu yabwino, ikuchita bwino ndipo nayo ikufunitsitsa chipambano komabe ifeyo tili pakhomo zomwe zikutilimbitsa mtima kuti tipambana masewerowa." Anatero Mkandawire.
Atakumana mchigawo choyamba ku Karonga, Chitipa inapambana 2-1 ndipo ngati apambane lero afika pa nambala yoyamba mu ligi pomwe Bangwe ifika pa nambala yachisanu, kutsala ndi mapointsi awiri kuipeza Silver Strikers.
Bangwe 2 chitipa 1
🇧🇷 Anthony is dropped from the Brazilian National Team at the request of the CBF, after being reported for gender violence. In his place, they summon Gabriel Jesús.
Official statement 👇🏻
“In light of the facts which came to light on Monday concerning Manchester United player Antony, which must be investigated, and in order to safeguard the alleged victim, the player, the Brazilian national team and the CBF, the organization informs that the athlete has been removed from the Brazilian national team”.
MUNTHALI SAKUPEZEKABE KU LEOPARDS
Katswiri wa timu ya Flames, Brighton Munthali, sakupezekabe kutimu ya Black Leopards kwa masabata awiri tsopano pomwe sabata ino sanapezeke pa masewero omwe timuyi inagonja 1-0 ndi Casric Stars mu Motsepe Foundation Championship.
Katswiriyu sanapezeke mmasewero oyamba pomwe timuyi inasewera ndi Pretoria Callies sabata yapitayo.
Katswiriyu anapita kutimuyi miyezi itatu yapitayo ndipo anatsatira wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Peter Mponda.
TEMWA WAFIKA ZIGOLI 20 KU CHINA
Katswiri wa timu ya Scorchers, Temwa Chawinga, wafikitsa zigoli 20 mu ligi ya amayi ku China pomwe loweruka latha anamwetsa zigoli ziwiri kuti Wuhan Jiangda iphe Shandong 3-0.
Katswiriyu ali pafupi potenga mphoto yogoletsa zigoli zambiri yachitatu mu chaka chino pomwe wakutsogola ndi zigoli 9 pamwamba pa akatswiri omwe amwetsa zigoli zochuluka.
"LIGI YATENTHA KOMA TILIMBIKIRA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati ligi ya TNM Supa ligi yatentha kwambiri pomwe zotsatira zikumakhala zozondoka koma ayesetsa kuti apeze zipambano zochuluka mu ligiyi.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Moyale Barracks 1-0 ku Rumphi ndipo wayamikira anyamata ake kamba ka chipambanochi.
"Anali masewero otentha kwambiri koma tiyamikira anyamata kuti apeza chipambanochi, mmene tinawauzira kuti tipeze chigoli mu mphindi 15 zoyambilira anapangadi." Anatero Chirwa.
Mphunzitsiyu watinso timu yake ikuyenera kupambana mmasewero awo akubwera kutsogoloku kuti adzamalize pabwino kamba koti ligiyi yatentha kwambiri. KB yafika pa nambala yachisanu ndi mapointsi 28 pa masewero 20.
"OYIMBIRA AKUMATENGA MBALI PA MASEWERO" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati oyimbira mmasewero awo ndi Karonga United anatenga gawo lina lolepheretsa kuti apambane koma kutenga point imodzi koyenda ndi chamuna.
Kananji amayankhula izi atatha masewerowa omwe matimuwa analepherana 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo wayamikira osewera ake kamba kozipereka mmasewerowa.
"Tithokoze Mulungu kuti tasewera ndi Karonga United, tiwayamikirenso anyamata athu agwira ntchito yotamandika, tinabwera ndipo tinayesetsa kuti mwina tipeze chipambano komabe achina Newton akumatenga mbalinso yaikulu bola asamakhale ndi mbali." Kananji anafotokoza.
Iye wati point yomwe atenga mmasewerowa iwathandize kupita patsogolo ndipo wati pang'onopang'ono akhale akuyendabe kuthawa chigwa cha matimu otuluka. Eagles yafika pa nambala 13 ndi mapointsi 21 mmasewero 20.
"NGAKHALE KU MANGALANDE MATIMU AKUMUNSI AMAVUTA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United wati masewero awo ndi Blue Eagles anali ovuta kwambiri kutengera kuti Eagles ili kumunsi ndipo matimu oterewa amavuta kulikonse.
Mphunzitsiyu amayankhula izi atatha masewero omwe matimuwa afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake yasewera bwino kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti anzathuwa akuthawa kumunsi kuja nde tinadziwa kuti abwera mwa mphamvu komabe anyamata anayesetsa komabe ngakhale ku England, timu imene ili kumunsi olo ikamasewera ndi Manchester United imavuta." Anatero Kajawa.
Iye wati akufunitsitsa kupeza zipambano zochulukabe kuti akhale pa nambala yabwino ikamatha ligi ya chaka chino. Karonga yaimabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi 28 pa masewero 21.
"PALIBE PHUMA POTI TIMAYANG'ANA TOP 8" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati timu yake ilibe phuma lililonse kamba ka kugonja ndi timu ya Mighty Wakawaka Tigers kamba koti iwo samayang'ana kwambiri ukatswiri wa ligi koma akhale mu matimu 8 oyambilira.
Mtetemera amayankhula izi atatha masewero omwe anagonja 2-1 ndi Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira Tigers kamba kopambana komanso kuti akonza mavuto awo.
"Leroli tinavutika kumbuyo chifukwa tangopereka zigoli zija koma kupita mmasewero ndi Bangwe, adzakhalanso ovuta koma tikonze mavuto athu. Palibepo phuma lililonse chifukwa ife timayang'ana top 8 nde zikutheka ndithu." Mtetemera anafotokoza.
Kutsatira kugonjaku, Chitipa yakanika kuti ifikebe pamwamba pa ligi pomwe yakhalabe ndi 36 points pa masewero 20 tsopano ndipo ali pa nambala yachitatu mu ligi.
"OSEWERA SAKUFUNA KUMVA ZOMWE TIKUKAMBA" - CHINGOKA
Mmodzi mwa aphunzitsi kutimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati osewera atimuyi akuvutika chifukwa sakudekha akafika pagolo zomwe zikupangitsa kuti ataye mipata yochuluka kwambiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 1-0 ndi Kamuzu Barracks ndi chigoli cha Olson Kanjira pa mphindi 8 ndipo iye wati anyamata ake sakumvera zimene aphunzitsi akuwauza.
"Anali masewero ovuta kwambiri ndipo tagonja koma kaseweredwe kanali kabwino, kupeza mipata koma kutsogolo kwathu ndi kumene kukuvutika chifukwa anyamata sakudekha nde akungophonya, mwina sakufuna kumvera zomwe tikuwauza." Anatero Chingoka.
Timu ya Moyale yavutika ndi zotsatira mmasewero angapo ndipo tsopano ili pa nambala 12 ndi mapointsi 23 pa masewero 20 omwe yasewera.