PETER BANDA WABWERERA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti yasaina katswiri wawo wakale, Peter Banda, kuti atumikirenso kutimuyi.
Izi zadza pomwe iye wathetsa mgwirizano wake ndi timu ya Simba SC ndipo tsopano wapanga chiganizo chotumikiranso timuyi.
Katswiriyu anapita kutimuyi mu 2019 komwe anathandizira timuyi kutenga chikho cha TNM komanso anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba kuposa onse mu ligi.
Izi zinachititsa kuti timu ya Sheriff Tiraspol yaku Georgia imutenge pa ngongole ya miyezi isanu ndi umodzi ndipo atachokako, timu ya Simba inamutenga koma amavutika kamba kuvulala kwambiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores