"TIMUSOWA FODYA MMASEWERO ENAWA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timuyi imusowa katswiri wawo, Yamikani Fodya, yemwe sapezeka mmasewero awo a ndime Ina yomwe akumane ndi TP Mazembe mu CAF Champions league kamba koti anapatsidwa kalata yofiira dzulo mmasewero awo ndi Dragon.
Katswiriyu analandira chikalatachi anaponda osewera wa Dragon komabe timuyi inapambana masewerowa 1-0 kuti afike mu ndime yachiwiri yachipulula ya chikhochi 3-0 pa zigoli zonse. Munthali anati timu yawo inataya mipata kwambiri ndipo azikonza mmasewero akubwerawa.
Iye anatinso Fodya wakhala ofunikira kwambiri kutimuyi komabe kusapezeka kwake kuwapangitsa kuti ena awagwiritse ntchito mmasewero akudzawa.
"Zoonadi Fodya wakhala wofunikira masewero athu makamaka ndi ukadaulo omwe ali nawo ndipo kusapezeka kwake timusowa koma tili ndi anyamata ena omwe tiwakodole kuti agwire ntchito, tinali nawo ena anavulala ndipo apa agwira ntchito." Anatero Munthali.
Bulle
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores