"UKADAULO WA PETER BANDA UTITHANDIZA MU CAF" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati kubwereranso kwa katswiri wa Flames, Peter Banda, kutimuyi kuwathandiza kuti aonjezere mphamvu mu CAF Champions league ndi zikho za mdziko muno.
Iye amayankhula izi pomwe katswiriyu amasaina mgwirizano wake wa miyezi inayi ndipo Munthali wati akukhulupilira kuti Banda ndi osewera yemwe Bullets idalire kwambiri mmasewerowa akuluakulu.
"Ndi zoona kuti Peter Banda wabwerera ku Bullets atathetsa mgwirizano wake ndi Simba, kubwera kwake kutithandiza makamaka ndi ukadaulo omwe ali nawo omwe watenga ku Simba yomwenso imasewera mu CAF nde arithandizira kwambiri mmasewero ngati amenewa." Anatero Munthali.
Iye wati katswiriyu akuyenera kulimbikira kutengera kuti anyamata ena omwe wawapeza kutimuyi nawo akuchita bwino. Banda wachoka kutimuyi kutsatira kusapeza mpata wosewera pomwe anakumana ndi vuto lovulalavulala.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores