"SITINAFIKEPO" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake sinafikepo pomwe akuyang'ana zokumana ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Karonga lamulungu.
Kajawa wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati masewero ndi Blue Eagles ndi osiyana ndipo akuyenera kuwatenganso mosiyana komanso osawaderera.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti Eagles ndi timu Ina yabwino, tisawaphweketse chifukwa ali kumunsi koma tikuyenera kuti tiwalemekeze ndikukasewera kuti tipambane"
"Sitikutengera kuti tinawagonjetsa 1-0 pa kwawo kapenaso kuti tikupambana ayi, tisakomedwe ndipo sitinafikepo, tikuyang'anabe masewero aliwonse paokha." Anatero Kajawa.
Karonga ili pa nambala 6 ndi mapointsi 27 pa masewero 20 ndipo sinatayeko mapointsi pansi pa Kajawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores