CIVO YAKONZEKA KUGWETSA BULLETS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake ndi yokonzeka kukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe matimuwa atengerane ku ndewu yamu TNM Supa ligi lachitatu pa bwalo la Kamuzu.
Chidati amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati mkhope zonse mutimuyi zikuoneka zokonzekera masewerowa ndipo wati zomwe akupitira ndi chipambano.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tikukumana ndi timu Ina yabwino komabe mpira umapanga zimene ziliko tsiku limenelo, ife tikayesetsa kuti tikapeze zotsatira zabwino." Anatero Chidati.
Iye wati timuyi ilibe yemwe ali ovulala patsogolo pa masewerowa ndipo wati anyamata akonzeka kwambiri. Civo ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe yatolera mapointsi 24 mmasewero 18.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores