BANDA WASIYANA NDI SIMBA
Katswiri wa timu ya Flames, Peter Banda, tsopano ali ndi ufulu wopita ku timu iliyonse pomwe timu ya Simba SC yalengeza kuti yasiyana ndi katswiriyu.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lolemba pomwe timuyi yathokoza katswiriyu kamba kokhala ndi timuyi mu zaka ziwiri kutsatira kumusaina kuchokera ku FCB Nyasa Big Bullets mu 2021.
Banda wavutika kuti akhazikike kutimuyi pomwe amangovulala nthawi zambiri kupangitsa kuti asewera masewero ochepa ngakhale kuti amakondedwa kutimuyi.
Zamveka kuti osewerayu akhonza kubwereranso ku Bullets pomwe akufuna kuzitolera kuti azigulitsenso kunja kwa dziko lino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores