IDANA SAPEZEKA NDI GUINEA
Katswiri wa timu ya Flames, Chimwemwe Idana, sapezeka mmasewero omwe timuyi ikumane ndi Guinea pa 10 September kamba koti ali ndi makalata achikasu awiri omwe anawatenga mmasewero ndi Egypt komanso Ethiopia mmiyezi iwiri yapitayo.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi lomwe latsimikiza za nkhaniyi pomwe timuyi yayamba zokonzekera zawo lolemba ndipo Idana anali konko.
Katswiriyu wapita kutimuyi ngati opanda timu pomwe zomwe amafuna kuti apite ku Zambia zikuvuta ndipo tsopano ali ndi mwayi osewerera Mbeya City yokha yomwe inatuluka mu ligi yaikulu ku Tanzania.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores