"ODWALA TOKHATOKHA TAKUMANA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati masewero awo ndi timu ya Extreme FC masana a lachiwiri akhale ovuta poti matimu onse akufunitsitsa kutsala mu ligi koma ali kunsi kwa ligi.
Nyambose wayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati ngakhale kuti zinthu zikuvuta, timu yake ikupita mmasewerowa ndi cholinga chopambana mmasewerowa kuti achoke kumunsi kwa ligi koma watibe wakufa saopa kuola.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse takhalitsa ku mzere ofiira nde tikamakumana chonchi zimavuta komabe ifeyo takhalitsa kumene kuja, tikufunitsitsa titachokako kumene kuja kuti tifikire ku mtundako nde anyamata tawauza kufunikira kopambana masewero amenewa." Anatero Nyambose.
Iye wati masewerowa awatenge ngati a ndime yotsiriza poti sipabweranso ena kudzakumana ndi Extreme. Tigers ikuchokera kogonja 3-1 ndi Blue Eagles ndipo ili pa nambala 13 ndi mapointsi 18.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores