"TIKUONONGA NDALAMA POMWE OYIMBIRA AKUONONGABE ZINTHU" - MAPASULA
Mmodzi mwa akuluakulu ophunzitsa timu ya Red Lions, Chifundo Mapasula, wadandaula ndi oyimbira yemwe anali pa masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos ponena kuti watengapo mbali kuti timu yake igonje mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero awo omwe agonja 2-0 ndi timu ya Dedza Dynamos ndipo wati mchitidwe wa oyimbira ukusokoneza matimu ambiri mdziko muno.
"Oyimbira watengapo mbali sinali penate, osewera uja mpira unamumenya pa phewa koma apereka penate zomwe zikuchitikazi akutipondereza kwambiri chifukwa tikugwiritsa ntchito ndalama tikamasewera mpirawu koma oyimbira akumakhala ndi matimu nde nzosokoneza." Anatero Mapasula.
Iye anati timuyi inalinso ndi mavuto ena ochepa omwe akonze patsogolo pa masewero awo otsatira. Lions ili pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores