"AKANATIPATSA MASEWEROWA KUMAPETO A SABATAYI" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wadandaula ndi mmene masewero akuwapezera ponena kuti masewero awo ndi Civo United akanapatsidwa kumapeto kwa sabatayi osati lachitatu kuti osewera apumeko.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake sinapange zokonzekera zokwana komabe akonzeka kukakumana ndi Civo.
"Ndi zoonadi kuti masewero akutipeza pafupifupi, apa tinali ndi masewero mu CAF Champions league kenako lolemba anyamata anapuma pomwe sanapange zokonzekera ndipo lachiwiri anangoziongola nde masewero awa mwina akatipatsa kumapeto kwa sabata ino poti sitinapatsidweko masewero aliwonse." Anatero Munthali.
Iye wati masewerowa akhala ovuta kutengera kuti Civo amavutitsana nawo koma akudziwa kufunikira kopambana masewerowa. Chaka Chatha, pa bwalo pomwepa matimuwa analepherana 1-1 ndipo zinathanso motero mchigawo choyamba.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores