KAMWENDO WAKHUTIRA NDI POINT IMODZI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati ndi okhutira ndi kufanana mphamvu kwa timuyi ndi Moyale Barracks koyenda pamene wati pointi yomwe atengayo yawathandiza kusunthira kumtunda kwa ligi.
Kamwendo amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Rumphi pomwe matimuwa analepherana 1-1 ndi zigoli za Gastin Simkonda komanso Kondwani Chilembwe. Iye anayamikira timu yake kuti inasewera bwino.
"Tasewera bwino kwambiri mwina mchigawo choyamba timavutikirabe pang'ono koma ndasangalala ndi mphamvu zomwe osewera anaika mchigawo chachiwiri mpaka tapeza chigoli, kuphonya ndi ntchito yathu kuti tiwakonze koma achita bwino ndithu." Anatero Kamwendo.
Timuyi tsopano ili pa nambala 6 mu ligi ndi mapointsi 25 pa masewero 19 ndipo akusewera masewero awo otsatira lachitatu pomwe akumane ndi Ekwendeni Hammers pa bwalo la Rumphi lomweli.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores