KAONGA WAMWETSA CHOYAMBA CHA CHAKA CHINO
Katswiri wa Flames, Chawanangwa Kaonga, wagoletsa chigoli chake choyamba mu ligi ya MTN Super League yaku Zambia pa masewero omwe timu yake yalepherana 1-1 ndi FC Muza lachitatu.
Kaonga anamwetsa pa mphindi 40 mchigawo choyamba kuti ZANACO itsogole komatu Muza inabwenza pa mphindi 52 za masewerowa kudzera pa penate.
Timu ya Zanaco tsopano ili ndi ma points awiri pa masewero awirinso omwe yasewera kamba koti yafananitsa mphamvu mmasewero onsewa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores