MHANGO WAYAMBAPO
Katswiri wa Flames, Gabadinho Mhango wagoletsa chigoli chake choyamba kutimu ya Moroka Swallows pomwe timuyi yapha Cape Town Spurs 3-1 mu DSTV Premiership dzulo ku South Africa.
Mhango yemwe anapatsidwa mpata oyamba mmasewerowa anapita mpira kudzera pa free kick kuti apeze chigoli chachitatu cha timuyi mchigawo choyamba.
Iye wafika kumene kutimuyi kuchokera ku Amazulu yomwe inathetsa mgwirizano wake pomwe ligi ya mdzikomo inatsala pang'ono kuyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores