BANDA WAPITIRATU KU FLAMES
Katswiri yemwe wabwerera kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Banda, wakalowa mu m'bindikiro wa Flames patangotha maola ochepa atasewera masewero ake oyamba ku Bullets.
Katswiriyu anasewera mphindi 45 za masewero omwe Bullets inachita kuchokera kumbuyo kuti igonjetse Civo United 3-2 ndipo anatenga gawo lalikulu kuthandiza chigoli chachiwiri.
Iye ayamba nawo zokonzekera za timuyi lero pomwe akukonzekera masewero atimu ya Flames ndi Guinea mmasabata awiri akudzawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores