KONDOWE ALIMBIRANA PA MPHOTO YAKU BULLETS
Katswiri watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, apikisana nawo pa mphoto ya osewera omwe asewera bwino mu mwezi wa August angakhale kuti sanayambeko masewero mu TNM Supa ligi.
Kondowe wakhala ofunikira kwambiri ku timuyi mu mweziwu pomwe anagoletsa zigoli zofunikira kwambiri zimene zapulumutsa timuyi kuti isagonje kapenanso kuipambanitsa.
Iye anamwetsa chigoli chofunikira kuti Bullets igonjetse Extreme FC mu FDH Bank ndipo anagoletsanso ndi Mighty Wakawaka Tigers kuti matimuwa afanane mphamvu 1-1, chigoli chogonjetsera Dragon FC mu CAF Champions league komanso chigoli chachiwiri pomwe Bullets inagonjetsa Civo United 3-2.
Enanso omwe apikisane pa mphotoyi ndi katswiri wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa ndi wapakati, Chawanangwa Gumbo.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores