BULLETS YALEMBETSA PETER BANDA MU CAF
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yamulembetsa katswiri wawo, Peter Banda, pa osewera omwe akutumikira timuyi mu mpikisano wa CAF Champions league.
Mkulu oyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati kupezeka kwa katswiriyu mmasewerowa kudzathandizira kupha mwa nkhanza timu ya TP Mazembe yomwe akumane nayo kawiri mmwezi uno.
Katswiriyu anabwereranso ku Bullets kumapeto a mwezi watha kutsatira kuthetsa mgwirizano wake ndi timu ya SC Simba yaku Tanzania ndipo wasewera masewero amodzi kale ku Bullets omwe inapha Civo United 3-2.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores