"PALIBE PHUMA POTI TIMAYANG'ANA TOP 8" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati timu yake ilibe phuma lililonse kamba ka kugonja ndi timu ya Mighty Wakawaka Tigers kamba koti iwo samayang'ana kwambiri ukatswiri wa ligi koma akhale mu matimu 8 oyambilira.
Mtetemera amayankhula izi atatha masewero omwe anagonja 2-1 ndi Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira Tigers kamba kopambana komanso kuti akonza mavuto awo.
"Leroli tinavutika kumbuyo chifukwa tangopereka zigoli zija koma kupita mmasewero ndi Bangwe, adzakhalanso ovuta koma tikonze mavuto athu. Palibepo phuma lililonse chifukwa ife timayang'ana top 8 nde zikutheka ndithu." Mtetemera anafotokoza.
Kutsatira kugonjaku, Chitipa yakanika kuti ifikebe pamwamba pa ligi pomwe yakhalabe ndi 36 points pa masewero 20 tsopano ndipo ali pa nambala yachitatu mu ligi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores