MKANDAWIRE WATAYIRA KAMTENGO CHIKOOKA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake yagonja mmasewero awo ndi timu ya Chitipa United chifukwa choti goloboyi wa Chitipa United, George Chikooka, anali bwino kwambiri.
Mphunzitsiyu amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Mpira ndipo wati timu imene imataya mimwayi yochuluka imavutika kuti ipeze zigoli mpake yagonja.
"Tinapeza mipata yochuluka koma takanika kupeza zigoli nde timu imene imakanika kugoletsa zimavuta kupambana, anzathuwa anangopeza mipata iwiri agwiritsa ntchito. Leroli George Chikooka anadzuka bwino, timuyamikire ndithu wagwira ntchito yapamwamba." Anatero Mkandawire.
Iye wati timu yake ichilimikabe kuti ipeze zipambano mmasewero akutsatirawa kuti amalize pabwino mu ligi. Bangwe ikadali panambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapointsi 28 pamasewero 21.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores