MUNTHALI NDI CHAWANANGWA SAPEZEKA KWA MASABATA ATATU
Osewera awiri atimu ya Flames omwe amasewera kunja kwa dziko lino, Chawanangwa Kaonga ndi Brighton Munthali akhala masabata atatu asakugunda mpira kamba koti anavulala mmasewero omwe timuyi yalepherana 2-2 ndi Guinea loweruka pa bwalo la Bingu.
Munthali anavulala mchigawo choyamba ndipo anasinthana ndi Clever Nkungula pomwe Chawanangwa anavulala mu nthawi yoonjezera atagundana ndi osewera a Guinea.
Osewera onsewa athandizidwa ndipo auzidwa kuti asasewere kwa masabata atatu ndipo akaunikidwanso akapita ku matimu awo. Chawanangwa amasewera timu ya ZANACO ku Zambia pomwe Munthali ndi goloboyi wa Black Leopards yaku South Africa.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores