"TILI PAKHOMO TIKUYENERA KUPAMBANA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati masewero atimu yake akhale ovuta masana a tsiku la lero pomwe akukumana ndi Chitipa United koma wati apanga zothekera kuti apambane.
Mkandawire wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Mpira ndipo wati timu yake ikuyenera kugwiritsa ntchito mwayi wa pakhomo.
"Awa ndi masewero enanso ovuta pomwe Chitipa ndi timu yabwino, ikuchita bwino ndipo nayo ikufunitsitsa chipambano komabe ifeyo tili pakhomo zomwe zikutilimbitsa mtima kuti tipambana masewerowa." Anatero Mkandawire.
Atakumana mchigawo choyamba ku Karonga, Chitipa inapambana 2-1 ndipo ngati apambane lero afika pa nambala yoyamba mu ligi pomwe Bangwe ifika pa nambala yachisanu, kutsala ndi mapointsi awiri kuipeza Silver Strikers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores