"NGAKHALE KU MANGALANDE MATIMU AKUMUNSI AMAVUTA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United wati masewero awo ndi Blue Eagles anali ovuta kwambiri kutengera kuti Eagles ili kumunsi ndipo matimu oterewa amavuta kulikonse.
Mphunzitsiyu amayankhula izi atatha masewero omwe matimuwa afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake yasewera bwino kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti anzathuwa akuthawa kumunsi kuja nde tinadziwa kuti abwera mwa mphamvu komabe anyamata anayesetsa komabe ngakhale ku England, timu imene ili kumunsi olo ikamasewera ndi Manchester United imavuta." Anatero Kajawa.
Iye wati akufunitsitsa kupeza zipambano zochulukabe kuti akhale pa nambala yabwino ikamatha ligi ya chaka chino. Karonga yaimabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi 28 pa masewero 21.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores