NGINDE SAKUKONDWA KUKHALA PAMWAMBA PA LIGI
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati sichinthu chokondweretsa kwambiri kuti timu yake tsopano ili pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM pomwe wati cholinga chachikulu ndi choipanga timu kukhala yamphamvu.
Mphunzitsiyu amayankhula izi timu yake itapambana 2-0 ndi Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira ndi zigoli za kumapeto za Ghedo Lorenzo ndi Godfrey Kwiyokwa. Iye wati timu yake simadalira osewera mmodzi mpake atasintha timuyi inayamba kusewera bwino ndipo sakukondwa kwambiri pokhala pamtunda.
"Kwa ineyo sikuti ndine okondwa chifukwa cholinga chimene ndinapitira ku Chitipa ndi chokuti ndiyipange timu ija ikhale yamphamvu mu zaka ziwiri zikubwerazi nde kukhala pa nambala 1, aziyankhula ndi mapointsi osati nambala." Anatero Mtetemera.
Chipambanochi chinali chachiwiri koyenda ndipo chawafikitsa pa nambala yoyamba ndi mapointsi 39 pamwamba pa FCB Nyasa Big Bullets yomwe ikutsalira ndi masewero atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores