"OSEWERA SAKUFUNA KUMVA ZOMWE TIKUKAMBA" - CHINGOKA
Mmodzi mwa aphunzitsi kutimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati osewera atimuyi akuvutika chifukwa sakudekha akafika pagolo zomwe zikupangitsa kuti ataye mipata yochuluka kwambiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 1-0 ndi Kamuzu Barracks ndi chigoli cha Olson Kanjira pa mphindi 8 ndipo iye wati anyamata ake sakumvera zimene aphunzitsi akuwauza.
"Anali masewero ovuta kwambiri ndipo tagonja koma kaseweredwe kanali kabwino, kupeza mipata koma kutsogolo kwathu ndi kumene kukuvutika chifukwa anyamata sakudekha nde akungophonya, mwina sakufuna kumvera zomwe tikuwauza." Anatero Chingoka.
Timu ya Moyale yavutika ndi zotsatira mmasewero angapo ndipo tsopano ili pa nambala 12 ndi mapointsi 23 pa masewero 20 omwe yasewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores