"CHIPAMBANO CHINALI CHOFUNIKIRA KWA IFE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati chipambano cha timuyi chinali chofunikira kwambiri kuti aziyendabe bwino kugonjetsa timu ya Civo United 2-0 pa bwalo la Chitowe lachitatu lathali.
Stain Malata anamwetsa zigoli ziwiri mmasewerowa zomwe zathandiza timuyi kupambana ndipo Mwansa wati Civo inasewera mpira wapamwamba koma zigoli za changu zawathandiza kuti apambane.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa Civo yamenya bwino kwambiri komabe anyamata anayesetsa kutsekatseka monse kuti isadutse ndipo zigoli za changu zatithandiza kwambiri, timafunikira kuti tiwine ndithu kuti chitsogolo chikhale chowala." Anatero Mwansa.
Kutsatira kupambanaku, timu ya MAFCO yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 24 pa masewero 21 omwe yasewera. Masewero awo otsatira aliko lamulungu likudzali pa bwalo lomweli ndi Dedza Dynamos.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores