"ATITULUTSA NDI IWOWO KOMA SITINATULUKE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati anthu omwe akuti timuyi yatuluka kale mu ligi ya TNM akuyankhulira mmaganizo awo koma timuyi ikhalabe mu ligiyi.
Mwansa amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe timu yawo ikumane ndi Civo United pa bwalo la Chitowe ndipo wati timuyi ikuyenera kupeza chipambano mwa njira ina iliyonse.
"Akhala masewero ovuta kwambiri koma tikuyenera kuti tichite bwino chifukwa choti sitili pabwino, tili kumunsi nde chipambano chitithandiza kuti tifike kumtundaku. Ife mu ligi sitinatuluke, awo akuyankhulawo ndi maganizo awo koma adzayankhule ligi ikadzatha." Watero Mwansa.
Timuyi ili pa nambala 14 mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero 20 omwe yasewera. Akapambana, timuyi ifike pa nambala 12 ndi mapointsi 24.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores