ANYAMATA ANAYI ACHIRA, ATATU AKADALI OVULALA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets itha kukhala yokondwa kwambiri kamba koti idzakhala ndi anyamata ake anayi, Hassan Kajoke, Patrick Mwaungulu, Eric Kaonga ndi Precious Sambani mmasewero awo ndi TP Mazembe mu CAF Champions league poti iwo achira.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Heston Munthali, ndi yemwe wanena izi pomwe amayankhula ndi olemba nkhani akutimuyi pa nkhani mmene osewera alili.
Iye wati Mwaungulu, Kajoke ndi Kaonga apanga zokonzekera zonse ndi timuyi sabata yonse ndipo Sambani ayamba lolemba pomwe wati ali tsopano bwino. Osewera atatu, Stanley Biliati, Alick Lungu ndi Mike Mkwate sapezeka mmasewerowa.
Mkwate sapezeka kwa ligi ya chaka chino yonse pomwe Biliati ndi Lungu ayambapo mmasabata atatu akudzawa. Bullets ikumana ndi Mazembe lamulungu lapa 17 September pa bwalo la Bingu asanakakumanenso pakhomo pa Mazembe ku DRC.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores