Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Yohane
BANJA LA KHUDA NDI ENELECIO LATHA
Katswiri wa mpira wamiyendo, Khuda Muyaba, watsimikiza kuti wasiyana banja ndi katswiri wakale wa Scorchers, Enelecio Mhango, pa zifukwa zoti mkaziyu samakhulupilika pa banja.
Muyaba walemba nkhaniyi pa tsamba la Facebook pomwe wati Mhango amatuluka mnyumba kumakayenda ndi amuna ena nthawi yomwe Muyaba amasewera mpira ku South Africa komanso ku Syria komanso amachita zomwe mwini wake akuti uhule ku malo omwera mowa.
Awiriwa asiyana ali ndi ana aamuna awiri ndipo Khuda wati ndi okhumudwa kamba koti amamuchitira mkaziyu kalikonse.
#Tawonga2023
CHIKHO CHA NYASA CAPITAL FINANCE CHAKWERA NDI K5 MILLION
Kampani yobwereketsa ndalama ya Nyasa Capital Finance Limited yalengeza kuti ndalama zomwe zimapita ku chikho cha mpira wamiyendo cha kampaniyi chakwera kufika pa K70 million kuchoka pa K65 million.
Wapampando wakale wa kampaniyi, Fleetwood Haiya, walengeza izi pa mwambo wokhazikitsa mpikisanowu ku Lilongwe loweruka madzulo. Iye wati akuyembekeza kuti mpikisanowu uthandiza kuonetsa poyera maluso obisika mzigawo zonse.
Ndipo wapampando watsopano wa kampaniyi, Joseph Mononga, wati kampani yawo ipitilira kuthandiza chikhochi kwa zaka zopyolera zitatu zomwe akhalapo kale.
Mu chaka choyamba, chikho cha Nyasa Capital chinali pa K15 million , kenako K25 million chaka chachiwiri chisanafike pa K65 million chaka chatha.
OCHEMERERA A SILVER ANAMENYA A DEDZA DYNAMOS
Mpira wa pakati pa Silver Strikers ndi timu ya Dedza Dynamos unathera zipolowe pomwe ochemerera atimu ya Silver Strikers amagenda aliyense wa Dedza Dynamos kutsatira kugonja kwawo 1-0 pa bwalo la Champions ku Dowa.
Mmodzi mwa atolankhani omwe anali nawo ku bwaloli, Andrew Mdzumirah, anaona chilichonse ndipo wati mkulu wa achitetezo a Dedza Dynamos anavulazidwa kwambiri pomwe miyala ndi mabotolo amagendedwa kwa anthuwa.
"Inenso ndinali ndi nkhawa kuti mabotolo akuponyedwawa sandifika chifukwa masapota a Silver amagenda amene wavala zofanana ndi makaka a timu ya Dedza. Pa nthawiyi ineyo ndinavala bib ya Sulom yamakaka a chikasu. Nthawi yomwe ine ndimachoka pa bwaloli mkuti osewera komaso akuluakulu a timu ya Dedza Dynamos atangokhala m'bwaloli kuopa kumenyedwa." Analemba Mdzumirah.
Timu ya Dedza Dynamos inachita kuperekezedwa ndi khwimbi la apolisi kamba ka chipolowechi. Alex Benson ndi yemwe anamwetsa chigolichi pa mphindi 74 za masewero
OSEWERA A BULLETS ALANDIRA K0.2 MILLION ALIYENSE AKAPHA TP MAZEMBE
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalonjeza osewera awo kuti apatsidwa ndalama yoonjezera yokwana MK200,000 aliyense ngati agonjetse timu ya TP Mazembe masana a lamulungu pa bwalo la Bingu ku Lilongwe.
Mkulu oyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, wati osewera atimuyi akonzekera kwambiri kwambiri ndipo ndi zomwe apatsidwa, akonzeka kugwetsa Mazembe mu CAF Champions league. Iye wathokozanso osewera akale, Kinnah Phiri ndi Lawrence Waya kamba kodzawalimbikitsa osewerawa.
"Tili ndi chikhulupiliro kuti osewerawa agwira ntchito chifukwa chilichonse apatsidwa. [Kinnah ndi Lule] sitinawaitane koma anangoona okha kuti abwere adzawalimbikitse osewera athu, tikuwathokoza kwambiri." Anatero Chigoga.
TP Mazembe inafika mdziko muno lachinayi patsogolo pa ndime yoyamba ya masewero a CAF Champions league ndipo otsatira azachitika ku DRC konko.
"KUTENGA LIGI KUTIVUTA KOMA KUKHALABE MULIGIMU" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati wauza osewera ake kuti asagone chifukwa choti atuluka ku malo a matimu otuluka mu ligi koma akuyenera kuchilimbika kwambiri poti sali otetezekabe.
Iye amayankhula izi kutsatira kupambana 2-0 ndi timu ya Extreme FC pa bwalo la Nankhaka ndipo wati ndi okondwa kamba ka chipambanochi. Iye wapempha osewera ake kuti achilimike kuti akhalebe mu ligiyi.
"Mukuona mmene ligi yavutiramu sitili pabwinobe nde tawauza osewera kuti apeze zipambano mwina mmasewero atatu kapena anayi zimenezi zitha kutikhalira bwino." Anatero Chingoka.
Iye wati vuto lalikulu lili komwetsa zigoli ndipo ayesetsa kukonza zinthuzi kuti izipeza zigoli. Moyale yafika pa nambala 11 pomwe ili ndi mapointsi 26 mmasewero 22 omwe asewera.
"OSEWERA AMALIMBIKIRA AKAMASEWERA NDI MATIMU AKULUAKULU" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati vuto losewera bwino akamakumana ndi matimu akuluakulu ndi limene lawapweteketsa mu ligi ya TNM.
Kafoteka amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Moyale Barracks yomwe inali ndi osewera mmodzi olandira kalata yofiira pa bwalo la Nankhaka. Iye wati timu yake imaphonya kwambiri.
"Anali masewero abwino kwambiri makamaka mchigawo chachiwiri chomwe timasewera bwino koma anyamata aphonya kwambiri mwina zigoli zitatu kapena zinayi. Vuto anyamata amaganiza ngati ochinya ndi wakutsogolo yekha koma timawauza kuti aliyense kaya wakumbuyo atha kugoletsa." Anatero Kafoteka.
Iye anatinso timu yake ikuyenera kusewera mofanana mmasewero awo onse pomwe wati amatsitsa moto akamakumana ndi matimu ocheperako kusiyana ndi matimu akuluakulu.
Timuyi ili pa nambala 16 pomwe ili ndi mapointsi 14 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
"NDI ZOKHUMUDWITSA NDIPO SIZINGAPITITSE MPIRA PATSGOLO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati ndi wokhumudwa kamba koti ochemerera atimu yawo anagendedwa ndikuvulazidwa ndi ochemerera atimu ya Silver Strikers ndipo wati sizoyenerera mu mpira.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Silver 1-0 ndipo anati ndi wokondwa ndi mmene anyamata anasewerera pa bwalo la zamasewero koma zoti ena anagendedwa ndi zokhumudwitsa.
"Anyamata asewera bwino, mchigawo choyamba mwina timakanika kusewera bwino timamenya mpira wammwamba koma mchigawo chachiwiri tinasintha ndipo tinayamba kupanikiza mpaka kupeza chigoli, tasewera ngati timu lero tiwayamikire anyamata koma ena agendedwa zomwe zili zokhumudwitsa." Anatero Chirwa.
Chipambano cha timuyi chaitengera pa mapointsi 29 pomwe yafika pa nambala 8 ndipo wasewera masewero 21. Bungwe la Super league of Malawi silinayankhulepo za chipolowechi.
"TIKUYENERA TIPAMBANE MMASEWERO ONSE ATSALAWA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati za kugonja kwawo ndi Dedza Dynamos zapita ndipo akuyang'ana za kutsogolo pomwe akufuna kupambana mmasewero awo onse omwe atsala mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewerowa omwe anagonja 1-0 pa bwalo la Champions ndipotu wati kuphonya kwambiri ndi kumene kwawaluzitsa mmasewerowa.
"Tinali ndi mipata yambiri yomwe takanika kugoletsa makamaka mchigawo chachiwiri koma basi tagonja 1-0 tikuyenera kuyang'ana chitsogolo kuti mwina masewero atsalawa titolere mapointsi atatu iliyonse." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers inaona katswiri wawo, Chimwemwe Idana, akupezeka makamaka mchigawo chachiwiri komabe sizinaletse Dedza kupambana. Silver ikadali pa nambala yachinayi pomwe ili ndi mapointsi 36 pa masewero 21.
"MASEWERO ATSALA ANGAPO, TIYAMBA KUCHITA BWINO" - NDAWA
Mphunzitsi watimu ya Red Lions, Franco Ndawa, wati ochemerera atimuyi asataye mtima kuti mwina timuyi ituluka pomwe wati kwatsalabe masewero omwe atha kuwapulumutsa mu ligi.
Ndawa amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pakhomo ndi Bangwe All Stars ndipo wati timu yake imaphonya kwambiri mipata yochuluka komabe ayesetsa kuzitolera kutsogoloku.
"Tinayesetsa kukonza mavuto athu osagoletsa koma kubwera mmasewerowa taphonya kwambiri kenako tayamba kuchinyitsa. Zinthu zikuvuta tivomereze koma masewero alipo angapo ngakhale akupita komabe tiyesetsa kuchita bwino mmasewero enawa." Anatero Ndawa.
Timu ya Red Lions ikufunika mapointsi okwana asanu ndi imodzi (6) kuti ituluke mu chigwa cha matimu osatuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 21 omwe yasewera.
"SAIZI ALI NDI LUSO LOSAKAKAMIZA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wayamikira katswiri wawo, Robert Saizi, kuti ali ndi luso lamtengo wapatali pomwe wati ndi osewera ofunikira kwambiri kutimuyi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Red Lions 2-0 pa bwalo la Balaka ndipo Saizi anatenga mphoto yoti wasewera bwino pomwe anagoletsa chigoli chachiwiri mmasewerowa. Iye wati kupambana kwa timuyi ndi kofunikira kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa Red Lions inabweranso kuti ipeze chipambano koma tinawauza osewera kuti akhazikitse mtima pansi pomwe tipeze mwayipo tigoletse. Saizi ndi luso losowa kwambiri, zosachita kukakamiza ndipo tinamusowa kwambiri ndi Chitipa." Anatero Mkandawire.
Chipambano cha Bangwe All Stars chaifikitsa pa nambala 6 pomwe yatolera mapointsi 31 pa masewero 22 omwe yasewera.
JUSSA
IDANA WABWERERA KU SILVER
Katswiri wosewera pakati, Chimwemwe Idana, wabwereranso kutimu ya Silver Strikers pomwe wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri kuti akhalebe kutimuyi.
Katswiriyu amatumikira timuyi pomwe anali pa ngongole kuchokera ku timu ya Mbeya City koma anachokako mgwirizano wawo utatha.
Katswiriyu analowera mdziko la Zambia komwe amafuna kupita ku Kabwe Warriors koma zinakanika ndipo analibe timu.
Koma katswiriyu wapanga chisankho chotumikiranso timuyi komwe ali ndi zigoli zisanu ndi chimodzi (6) komanso anathandizira zigoli zisanu ndi ziwiri (7).
Yp five bg du
Hoye hoye
Noma mmh
Today
"ZIVUTE ZITANI MAWA TIKUSWA EXTREME" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati timu yake yakonzekera kuti apeze chipambano mmasewero awo ndi Extreme FC pomwe akufuna kuchoka ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi ya TNM.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Nankhaka ndipo wati mavuto omwe anali nawo okanika kugoletsa zigoli awakonza ndipo akonzeka kutchisa Fodya waku Mchinji.
"Takonza mmene timakonzekerera masewero aliwonse koma awawa tipita ndi cholinga kwambiri chifukwa sizikutiyendera mu ligi. Chomwe chimativuta ndi kupeza zigoli nde ndi zimene taunikirapo kwambiri ndipo anyamata tawauza kuti mwa njira iliyonse tikapambane. Extreme nayo ilinso kumunsi nde sibwera mwachibwana komabe tiyesetsa kuti tipambane." Anatero Chingoka.
Awa akhala masewero oyamba ngati mphunzitsi watimuyi a Chingoka ndipo ngati angapambane, iwo atuluka mu munsi kwa ligiyi. Moyale ili ndi mapointsi 23 pa nambala 14.
BREAKING
Timu ya Moyale Barracks yaimitsa ntchito mphunzitsi, Nicolas Mhango, kamba ka kusachita bwino kwa timuyi.
Izi zadziwika pa mkumano umene timuyi inali nawo yowunikira mmene timuyi ikuchitira komanso zifukwa zimene isakuchitira bwino.
Padakali pano, Victor Chingoka, yemwe ndi wachiwiri kwa Mhango, atsogolera timuyi pomwe ikukumana ndi Extreme FC loweruka pa bwalo la Nankhaka.
Mhango anatulutsa kale Bangwe All Stars mu chigawo choyamba ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe Moyale ili pa nambala 14 ndi mapointsi 23.
Source: VOL
"TIKUYENERA KUWINA MWA NJIRA ILIYONSE" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake inayiwala kale zakugonja kwawo ndi timu ya Chitipa United ndipo wati akuyenera kupambana mwa njira iliyonse ndi timu ya Red Lions.
Mkandawire wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Balaka ndipo wati akukhulupilira kuti akhala ovuta potengera kuti Red Lions ikumenyera nkhondo yoti itsale mu ligi koma iwo akufuna chipambano.
"Anyamata akonzeka ndipo chimene tikuyang'ana ndi kuti titapambana masewero amenewa omwe atifikitse pa mapointsi 31 omwe tikuyang'ana ndithu. Mu sabata yonseyi takhala tikukonza kumbali yomwetsa zigoli ndipo anyamata akagwira ntchito." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe ili pa nambala 7 mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi 28 pa masewero 21 omwe asewera mu ligiyi.
"DEDZA NDI TIMU YABWINO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati akukhulupilira kuti masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos pa bwalo la Champions ku Dowa akhala ovuta kamba koti timuyi ndi yabwinonso.
M'gangira wayankhula izi pomwe amayankhula ndi olemba nkhani patsogolo pa masewerowa ndipo wati akukasewera pa bwalo loti sanasewerepo koma akukhulupilira kuti akapambana.
"Ndi masewero ovuta poti Dedza ndi timu yabwino, sungangopita kuti ukatenga mapointsi utangokhala, ukufunika kulimbikira nde tikupita mmasewerowa titapambana ndi Moyale zomwe zikupereka molalo kwa osewera komanso kuti anagoletsa ndi osewera atatu osiyanasiyana, zikupereka chithunzi kuti aliyense atha kugoletsa." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver ikapambana masewerowa, ifika pamwamba pa ligiyi pomwe padakali pano ali ndi mapointsi 36 pa nambala yachinayi mmasewero 20.
NYONDO SAPEZEKA NDI SILVER
Timu ya Dedza Dynamos itha kukhalabe yovutika kupeza zigoli pomwe katswiri wawo, Clement Nyondo, sapezeka mmasewero awo ndi timu ya Silver Strikers kamba kovulala.
Mphunzitsi watimuyi, Gilbert Chirwa, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati Nyondo wangoyamba majowajowa koma sangapezeke mmasewerowa chimodzimodzi Limbani Phiri yemwenso ndi ovulala. Iye wati Joseph Balakasi ndiyemwe wachira koma wati masewero ndi Silver ndi ovuta.
"Sikoyamba kukumana nawo ndipo si zachilendo kukumana nawo komano tikudziwa kuti ali ndi timu yabwino, osewera abwino anagonjetsa Moyale ndi zigoli zambiri koma ife ngati Dedza tipita olimba mu mphamvu ndi mzeru." Anatero Chirwa.
Dedza Dynamos ili pa nambala yachikhumi pomwe ili ndi mapointsi 26 pamasewero makumi awiri (20) omwe yasewera. Ngati ali ovulala, Nyondo akutsogolabe ndi zigoli mu ligiyi.
Caf champions league 2023
SOUTH AFRICA YAPALAMULA MOTO WA MALAWI
Timu ya mpira wamiyendo koma wa amayi, The Scorchers, yaikidwa mu gulu A la mpikisano wa COSAFA Women's Championship pomwe yaikidwa limodzi ndi matimu a South Africa, Madagascar ndi Eswatini.
Izi zadziwika pa mayere omwe anachitika lachinayi pomwe matimu khumi ndi awiri ayikidwa mu magulu atatu. Timu ya Malawi ilowa mu m'bindikiro lamulungu kukonzekera mpikisanowu. Magulu onse ali motere
GULU A GULU B GULU C South Africa Zambia Namibia Malawi Mozambique Botswana Madagascar Angola Zimbabwe Eswatini Comoros Lesotho
Mpikisano wa chaka chino uchitikira ku Gauteng, mdziko la South Africa kuyambira pa 4 mpaka pa 15 October 2023.
CIVO YAPEZA UBALE NDI KAMPANI YA TREE BUSINESS SUPPLY
Timu ya Civo United yapalana ubwenzi ndi kampani ya Tree Business Suppliers Malawi Limited partners omwe asainirana mgwirizano wa zaka ziwiri kuyambira mu ligi ya chaka cha mawa.
Timuyi yalengeza za mgwirizanowu lachinayi atagwirizana za mgwirizanowu womwe timu ya Civo ithandize kutsatsa malonda a kampaniyi pomwe zovala za Civo zizilembedwa dzina la kampaniyi uku ikuthandiza kugula unifolomu, majuzi, zikwana ndi zina zambiri.
Kampaniyi yati thandizo lawo lizifikiranso ku matimu achisodzera atimuyi komanso timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi yatimuyi pofuna kuonetsa kukhazikika kwao pa thandizoli.
Mbali zonse ziwiri zati ndi zosangalala ndi mgwirizanowu womwe uthandize kutukula ntchito za mbali zonse komanso kulumikizitsa ochemerera ndi makasitomala a kampaniyi.
PAPA KU WANDERERS?
Zamveka kuti timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikukambirana ndi katswiri wawo wakale, Gerald Phiri Jr, kuti abwererenso kutimuyi.
Phiri alibe timu pomwe anasiyana ndi timu ya Al Hilal yaku Sudan ndipo wakhala asakusewera kwa nthawi tsopano.
Iye anachoka ku Wanderers mu 2014 pomwe anapita ku timu ya Dynamos yaku Zimbabwe asanalowere ku matimu aku South Africa.
TP MAZEMBE YANYAMUKA BWAKU MALAWI
Timu yaku Democratic Republic of Congo, ya TP Mazembe, yanyamuka kwawo kulowera mu dziko la mkaka ndi uchi, la Malawi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu CAF Champions league pa bwalo la Bingu.
Timuyi yalengeza za ulendowu pa tsamba lawo la Facebook ndipo akuyembekezeka kufika mdziko muno maola akudzawa pomwe masewero aliko lamulungu likudzali.
Fixture
HAAA! ZACHITIK LERO NDIMAYESA NGATI LERO TIGONA PATOP KOMA MANOMA ANZANGA KD ZIKUPASA CHILIMBISO KT TITENGA LEAGUER CHAKA CHINO KAPENA NEBA ANANENELERA LEAGUER ZOIPA KT AZITENGA YEKHA
"TIMAFUNA KUIMENYA WANDERERS KOMA OYIMBIRA SAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati oyimbira wayiteteza timu ya Mighty Mukuru Wanderers kuti isagonje ndi timu yake pomwe wati ziganizo zimakomera eni bwalowa.
Chirwa wayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yalepherana 1-1 ndi timu ya Wanderers ndipo wati chigoli cha Wanderers sichinalowe komanso ziganizo zina sizinali zokomera onse.
"Tasewera masewero, tinabwera kuti tiyimenye Wanderers koma oyimbira samafuna. Ziganizo zake zinali zokondera ngakhale mmene timayamba masewero komabe tinapeza chigoli ndipo mchigawo chachiwiri wapereka chigoli choti sichinalowe." Anatero Chirwa.
Timu ya Kamuzu Barracks ikuimabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 29 pa masewero 21 omwe yasewera chaka chino. Iyo yatenga mapointsi anayi pamwamba pa Wanderers mu ligi ya chaka chino.
#TAWONGA2023
"OYIMBIRA ANATIBALALITSA NDE TAGONJA" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wati oyimbira anasokoneza timu yake kuti igonje ndi timu ya Silver Strikers pomwe wati zigoli zoyamba za Silver sizinali zoyenera kukhala zigoli.
Mhango amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 4-1 pa bwalo la Bingu ndipo timu yake ndi imene inayamba kugoletsa koma Silver inamwetsa zinayi. Iye wati oyimbira anawabalalitsa osewera ake.
"Timu yanga inayamba bwino koma anakhumudwa ndi mmene oyimbira anachitira, chigoli choyamba sichinali penate ndipo chachiwiri sichimayenera kukhalanso chigoli nde zinawafoola osewerawa." Anatero Mhango.
Iye anati anayesetsa kuwauza osewera awo kuti achilimike kuti asewerebe ndikupeza mwayi otsalabe mu ligi pomwe ali pa nambala 14 ndi mapointsi 23 pa masewero 21.
"SITIKUYANG'ANA ZOTSALA MU LIGI KOMA TOP 8" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati chipambano chomwe timuyi yapeza chiwathandiza kubweretsanso mtima wopambana kwa osewera pomwe akuyang'ana zoyambiranso kuchita bwino mu ligi ya TNM.
Mauluka amayankhula izi pomwe timuyi yapambana koyamba mu chigawo chachiwiri pomwe yagonjetsa Extreme FC pa bwalo la Rumphi. Iye wati ndi okondwa kamba ka chipambanochi ndipo zibwenzeretsa mtima wopambana kwa osewera atimuyi.
"Ndife okondwa kamba ka chipambanochi chimene takhala tikuchifuna kwambiri, kupambana kwa lero kutithandiza kuti anyamata abweremo mzimu opambana poti pakatipa anasiya kuzikhulupilira. Sitikuyang'ana zotsala mu ligi komatu kutsala mu top 8." Anatero Mauluka.
Pa masewero 21 yomwe asewera atimuyi, Ekwendeni Hammers yapeza mapointsi okwana 28 ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8).
"ZA UKATSWIRI ZITAYENI IFE TIKUYANG'ANA CHITSOGOLO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati zoyankhula zokhudza ukatswiri wa chikho cha TNM zisakambidwe kaye pomwe timu yake ikuyang'ana kuti kutsogolo kwao kukhala motani.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa timu ya Moyale Barracks 4-1 pa bwalo la Bingu kuti abwenzere maganizo ofuna kulimbirana ukatswiri wa ligiyi. Iye wayamikira anyamata ake kamba kopeza chipambanochi.
"Ndife osangalala ndi chipambanochi, tinachinyitsa mwachangu koma anyamata anaazipereka ndipo anachilimika mwachangu, ndi zokondweretsa kuti tapeza chipambano chachikulu pakhomonso. Za kutenga ligi zitayeni kaye ife tikuyang'ana kutsogolo kuti tione masewero oti tipambane." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ikadali pa nambala yachinayi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 36 pa masewero 20 omwe asewera mu ligiyi.
"MWINA NDIVOMERE KOYAMBA KUTI TIKUTULUKA MU LIGI" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati zinthu zikuvuta tsopano kutimu yake ndipo wavomera kwa nthawi yoyamba kuti timuyi ikhonza kutuluka mu ligi.
Kafoteka amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonja 1-0 ndi timu ya Ekwendeni Hammers pa bwalo la Rumphi ndipo wati mulingo womwe anauyika kuti apambane mmasewero awo wachepa ndipo ndi zokaikitsa kuti atsalabe mu ligi.
"Mwina tivomereze kwa nthawi yoyamba kuti tikutuluka mu ligi chifukwa timawerengera kuti mwina masewero 7 kapena 8 kuti titsale mu ligi koma tsopano mwayi wathu wachepa, tikuyesetsa koma zikuoneka kuti zinthu zikuvuta tivomereze ndithu." Anatero Kafoteka.
Extreme FC ikubwerera kuchokera kumpoto kwa dziko lino opanda pointi iliyonse pomwe yagonja mmasewero awo omwe anali nawo. Timuyi ilibe ndi mapointsi 14 pa masewero 22 omwe yasewera.
Akuwina ndani ma gemu alelo a tnm super leaguer
Ma Banka tamwa wamkaka😘😁
Results today
Kd noma ikuwina
Kamuzu barrack vs mighty wandereres
blue eagles
Ctv
"MWANA WOPANDA KHALIDWE PAKHOMO, KUNJA SATENGEDWA" - MATAYA
Mmodzi mwa anthu otsatira nkhani zamasewero mdziko muno, Mussa Mataya, wati ndi zovuta kuti oyimbira amdziko muno azitengedwa pa mipikisano yaikuluikulu pa dziko lonse poti amadandaulidwa angakhale ndi kwawo komwe.
Mataya wayankhula izi kutsatirakusapezeka kwa oyimbira aku Malawi pa ndandanda wa oyimbira omwe asankhidwa ndi bungwe la CAF kuti akaphunzitse maphunziro apadera patsogolo pa mpikisano wa AFCON. Iye wati kuli zambiri zomwe oyimbira akufunika akonze.
"Ndikukhulupilira kuti sizachilendo chifukwa chiyambireni ligi ya chaka chino, matimu akungodandaulabe kamba kosaimbira bwino nde zimene zija zimapita patali ndipo zikutsekereza mi mwayi yawo kunjaku." Anatero Mataya ndi Owinna.
Oyimbira 75 ndi omwe akutenga nawo mbali pa maphunzirowa ndipo palibepo aliyense waku Malawi yemwe watengedwapo.
BULLETS RESERVE YAKANIKA KUBWERA PAMWAMBA
Akatswiri omwe akuteteza ligi yakummwera kwa dziko lino ya Thumbs Up Southern Region Football league, FCB Nyasa Big Bullets Reserve, akanika kufika pa mwamba pa ligiyi pomwe yagonja 2-0 ndi timu ya Waka Waka Tigers Reserve pa bwalo la Kamuzu lolemba masana
Timuyi inali ndi mwayi ofika pamwamba kutsatira kugonja kwa timu ya FOMO FC 1-0 ndi timu ya The Boys lamulungu ndipo inaona ngati kutulo pomwe Tigers yomwe ikuvutika mu ligi yawamenya pakhomo pawo pomwepo.
Timuyi yataya mapointsi asanu mmasewero awiri omwe yasewera mmasabata awiri apitawa pomwe anafanananso mphamvu ndi timu ya The Boys 1-1 sabata yatha.
FOMO ilamulirabe mu gulu B la ligiyi ndi mapointsi 29 pa masewero 13 pomwe Bullets Reserve ili pachiwiri ndi mapointsi 26 pa maseweronso 14, Ntopwa ili ndi 23 pomwe Zomba Airbase ili ndi 21 mu gulu lomweli.
MACHESO NDI FODYA APEZEKA POKUMANA NDI MOYALE
Timu ya Silver Strikers ikhala ndi anyamata ake awiri, Patrick Macheso komanso Mark Fodya pomwe akhale akukumana ndi timu ya Moyale Barracks mu ligi ya TNM lachitatu pa bwalo la Bingu.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Peter M'gangira, ndi yemwe watsimikiza za kupezeka kwa akatswiriwa omwe akhala asakusewera kwa masabata angapo kamba kovulala.
Iye wati timuyi yakonzeka kukumana ndi Moyale yomwe akuyang'ana kuti akabwenze chipongwe poti anawatulutsa mu chikho cha FDH Bank ndipo anafanana mphamvu 0-0 mu chigawo choyamba cha ligiyi.
Silver ikapambana ifika pa mapointsi 36 mu ligi ndipo itha kufika pa nambala yachitatu ngati timu ya Mighty Mukuru Wanderers itagonje ndi Kamuzu Barracks pa bwalo la Kamuzu.
Tnm super ligue malawi
NDAWINA NAWO MUSABATA YA DATE 4 TO 10 NDIYE MUNDITUMIZI NDALAMA YANGA PANAMBALA IYI 0981658760.
CIVO ILI NDI MKUMANO LACHITATU
Timu ya Civo United ikhala ndi mkumano lachitatu kuti ikaunikire za mmene timuyi isakuchitira bwino kutsatira kupezeka kumunsi kwa ligi ya chaka chino.
Mlembi wamkulu watimuyi, Edgar Chilipanjira, watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati akufuna kufufuza chimene chikuchititsa kuti timuyi isamachite bwino mmasewero awo.
Izi zabwera kutsatira kugonja masewero atatu otsatizana ndipo ali pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) pomwe yatolera mapointsi 24 pa masewero 21.
Mkumanowu ukhudza akuluakulu atimuyi, aphunzitsi komanso osewera atimuyi ndipo a Chilipanjira akukhulupilira kuti izi zithandiza kuyambiranso kuchita bwino.
"CIVO ITHERA MU TOP 8" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Oscar Kaunda, wati timu yake ithera mkatikati mwa matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi ya TNM angakhale kuti sakuchita bwino mmasewero awo.
Kaunda amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Blue Eagles pa bwalo la Champions ku Dowa. Iye wati timu yake ikuphonya mipata yambiri koma akonza mavutowa.
"Tikupeza mipata yochuluka koma tikukanika kuipanga zigoli tingobwerera kuti tikakonze ndipo tithera mu top 8. Anthu ankakaika mu chigawo choyamba chija koma tinathera pa nambala 7, apapanso tipanga zinthu." Anafotokoza Kaunda.
Timu ya Civo ili ndi point imodzi pamwamba pa malo opulumuka pomwe ili ndi mapointsi 24 pa masewero makumi awiri ndi amodzi (21) mu ligi ya chaka chino.
"MASEWERO AKADALIPOBE NDIPO TIYESETSA" - MKANDAWIRE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsa kulimbikira mmasewero khumi omwe atsala nawo kuti amalize ligi ya chaka chino ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligiyi.
Mkandawire amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo anati timu yake yaphonya mipata yochuluka. Iye wati ayesetsa mmasewero omwe atsala nawo kuti asatuluke mu ligi.
"Apapa zinthu zikuipadi komabe tidikire chifukwa masewero atsala angapo, ife tatsala ndi 10 nde tiyesetsa kuwauza anyamata kuti alimbikire ndi cholinga choti tichoke kumunsi komwe tiliko." Anatero Mkandawire.
Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe yakwanitsa kupeza mapointsi 18 pa masewero 20 omwe asewera mu ligi ya TNM.
"MPHECHEPECHE MWA NJOBVU SAPITAMO KAWIRI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati sakufunanso kuti timu yake ibwererenso kumunsi kwa ligi komwe iwo anali kamba koti mmene ligi yavutiramu palibe timu yomwe ili pa mtendere.
Nyambose amayankhula izi timu yake itafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) kutsatira kugonjetsa Red Lions 1-0 pa bwalo la Kamuzu. Iye anati timu yake sinasewere bwino koma zilibe ntchito pomwe pakadali pano chipambano nde chofunikira.
"Tiyesetsabe kuti tipitilize kupeza zipambanozi chifukwa mphechepeche mwa njobvu sapitamo kawiri, kumunsi kuja sitikufuna tibwererenso nde tiyesetsa kupambana mmasewero athu." anatero Nyambose.
Tigers yatsala ndi masewero asanu ndi atatu (8) kuti imalize ligi ya chaka chino ndipo yakwanitsa kutolera mapointsi 27 ndipo ali ndi mapointsi anayi pamwamba pa malo amatimu otuluka mu ligi.
"NDINANENA KALE KUTI BLUE EAGLES SINGATULUKE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, watsindika kuti timu yawo singatuluke mu ligi ya TNM ndipo anthu ayionanso ikusewera momwemu chaka cha mawa.
Kananji amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 1-0 ndi Civo ku bwalo la Champions ndipo wati masewero anali ovuta koma chigoli cha msanga chawathandiza. Iye wati anyamata ake tsopano akubweramo pa mmene amafunira.
"Chichitikireni mkumano wathu uja, tapambani iyiyi yachiwiri ndipo tafanana mphamvu imodzi zomwe zikusonyeza kuti anyamata akubweramo ndipo tichita bwino. Ndinanena kale kuti nzosatheka kuti timu yathu ikhonza kutuluka mu ligi." Anafotokoza Kananji.
Timu ya Blue Eagles ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe yatolera mapointsi okwana 24 pa masewero 21 omwe asewera.
🚨 Paul Pogba has tested positive for testosterone from a drugs test after Juventus vs Udinese. He has three days to produce a counter-analysis of the result. If found guilty, doping bans carry suspensions from playing lasting between 2-4 years. [Sport Mediaset]
KONDOWE WASEWERA MWAPAMWAMBA MU AUGUST KU BULLETS
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, wasankhidwa kukhala osewera yemwe wasewera bwino kuposa onse kutimuyi mu mwezi wa August pomwe walandira mavoti ochuluka kuchokera kwa ochemerera atimuyi.
Kondowe wagonjetsa wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa komanso wapakati, Chawanangwa Gumbo pa mavoti kuti atenge mphotoyi kamba kopulumutsa Bullets kangapo mu mwezi umenewu.
Iye wagoletsa zigoli zitatu mu mweziwu zomwe zinali zofunikira kwambiri kutimuyi ndipo mmasewero onse omwe wasewera mu mweziwu, onse amachokera panja.
Iye alandira kachikho kakang'ono ndi ndalama yokwana K100,000 kuchokera ku kampani ya Hubertus Clausius Insurance kamba kopambana mphotoyi.
"EXTREME ILI NDI ZONSE ZOYENERA KUTI ISATULUKE" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati iye akulimbabe mtima kuti timu yakeyi situluka mu ligi ya chaka chino pomwe wati zoyenereza zonse alinazo kuti amene nkhondo yotsala mu ligiyi.
Kafoteka wayankhula izi lamulungu pomwe timu yake inagonja 2-0 ndi Karonga United pa bwalo la Karonga ndipo wati kugonjako ndi chifukwa choti anyamata ake anatopa ndi kuyenda poti anafika tsiku lomwelo.
Iye koma wati akukhulupilira kuti timuyi situluka mu ligi ya chaka chino monga iye mphunzitsi koma zitengera osewera kulimbikira kwao.
"Zotuluka mu ligi tikhonza kumenyerabe nkhondo, ineyo ngati mphunzitsi ndikunenabe kuti sitikuluka mu ligi koma zitengera anyamata ngati atazipereke." Anatero Kafoteka.
Extreme ikuchepekedwa ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) kuti ipeze timu yomwe sili mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi pomwe yatsala ndi masewero asanu ndi anayi kuti amalize ligi ya chaka chino.