SAIZI NDI CHAZIYA AMWETSA ZIGOLI ZOYAMBA KU FLAMES
Osewera atimu ya Flames, Robert Saizi komanso Lawrence Chaziya, atsegula matumba awo azigoli kutimuyi pomwe anamwetsa chigoli chimodzi aliyense kuti Flames ilepherane 2-2 ndi Guinea pa bwalo la Bingu loweruka masana.
Saizi anamwetsa chigoli chake choyamba ndi timuyi pa mphindi 23 anamalizitsa mpira omwe Lanjesi Nkhoma anamenyetsa munthu mu masewero ake achisanu ndi timuyi. Malawi inagoletsetsa zigoli ziwiri mu mphindi zitatu pomwe Aguibou Camara komanso Saidou Sow anamwetsa zigoli pa mphindi 56 ndi 58 aliyense kuti Guinea itsogole 2-1.
Masewero akupita kumapeto, Saizi anamenya Kona yomwe Chaziya anasumbira mu ukonde kuti apezenso Chigoli chake choyamba ndi timuyi mmasewero ake achikhumi chomwe chaletsa Flames kugonja.
Mu gulu la timuyi, Flames yathera pachitatu ndi mapointsi asanu pa masewero asanu ndi amodzi ndipo Egypt ndi Guinea ndi omwe achoka mu gululi ndikupita ku mpikisano wa African Cup of Nations wa 2023.
#Tawonga2023
malawi tiyeni tilimbikikle
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores