"ANGAKHALE OMWE ALI PAMTUNDA SALI SAFE" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo, Wilson Chidati, wati ligi ya chaka chino ikuvuta kwambiri ndipo palibe timu imene ili pa mtendere mu ligi ya TNM ya chaka chino.
Chidati wayankhula izi patsogolo pa masewero a timuyi ndi MAFCO omwe aseweredwe pa bwalo la Chitowe ndipo wati timu yake ikuyenera kupambana kuti ikulitse mwayi womaliza bwino mu ligiyi.
"Akhala masewero ovuta kwambiri chifukwa ligi ya chaka chino akuvuta kwambiri ndipo palibe timu imene ili safe nde ukumati ukapeza point iliyonse, ikumakhala yofunikira kwambiri mu ligiyi. Takonzekera bwino lomwe kuti tikathe kupeza chipambano." Anatero Chidati.
Timu ya Civo ili pa nambala 10 mu ligi ya TNM pomwe ali ndi mapointsi 24 ndipo akapambana afikabe pa mapointsi 27.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores