"LIGI YATENTHA KOMA TILIMBIKIRA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, wati ligi ya TNM Supa ligi yatentha kwambiri pomwe zotsatira zikumakhala zozondoka koma ayesetsa kuti apeze zipambano zochuluka mu ligiyi.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Moyale Barracks 1-0 ku Rumphi ndipo wayamikira anyamata ake kamba ka chipambanochi.
"Anali masewero otentha kwambiri koma tiyamikira anyamata kuti apeza chipambanochi, mmene tinawauzira kuti tipeze chigoli mu mphindi 15 zoyambilira anapangadi." Anatero Chirwa.
Mphunzitsiyu watinso timu yake ikuyenera kupambana mmasewero awo akubwera kutsogoloku kuti adzamalize pabwino kamba koti ligiyi yatentha kwambiri. KB yafika pa nambala yachisanu ndi mapointsi 28 pa masewero 20.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores