"MWINA MATIMU TIZINGOSONKHERANA NKUMAIMBIRA TOKHA" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Oscar Kaunda, wadandaula kuti oyimbira wawaonongera masewero pomwe timuyi yagonja 2-0 ndi timu ya MAFCO ku bwalo la Chitowe lachitatu.
Kaunda anayankhula izi masewerowa atatha ndipo wati zigoli zimene Stain Malata anagoletsa zinali zowapatsa ndipo anasewera ndi phuma kuti abwenze zigolizo mpake anakanika kugoletsa mipata yomwe anaipeza.
"Tasewera bwino kwambiri koma mwina mipata sitinathe kuipanga zigoli, komanso mwina bola tizingosonkherana matimu nkumaimbira tokha kuti mwina oyimbirayo aziopa Civo ndi MAFCO chifukwa leroli ationongera masewero mu kanthawi kochepa." Anatero Kaunda.
Iye wati timu yake isewetsa kuti izitolere changu ndi cholinga choti masewero awo a lamulungu adzapambane ndi Blue Eagles. Civo ili pa nambala 11 ndi mapointsi 24.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores