Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"POINT IMODZI NDI YOLANDILIKA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati kupeza point imodzi pa masewero awo ndi Premier Bet Dedza Dynamos ndi zolandilika kusiyana ndikugonja ndipo wayamika osewera ake kamba kolimbikira kuti abwenze chigoli nthawi yothaitha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati anali ndi masewero ovuta poti Dedza inakonzeka kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri poti Dedza Dynamos ndi timu yabwino kwambiri ndipo inatidzidzimutsa ndi penate ija koma anyamata anayesetsa mpaka tabwenza, point imodzi ndi yabwino kusiyana ndi kugonja." Anatero Chirwa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi ndi chitatu (13) ndi mapointsi okwana 11 pa masewero khumi (10) omwe yasewera mu ligi yawo yoyamba ya TNM.
Takutumizirani nonse: Mondo 👏👏 Richman 👏👏
"WE HAVE A HUGE HOMEWORK" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Kalitso Pasuwa, said his team has a huge work to do in order to start getting positive results as their striking forcing is missing a lot of chances they are getting in their matches.
He said this after his team dropped yet other two points in their 1-1 draw against Creck Sporting Club at the Civo Stadium and said they need a players to be scoring as only Patrick Mwaungulu is scoring at the team.
"Remember, we are coming back from a loss and today we have picked a point and I think we need to do more in terms of how we hit the net but I think we are having so many chances but we are failing to take and we only have one boy who is scoring and we need everyone to be scoring so i think it's a home work for us coaches to sit down and look into this." Said Pasuwa.
The People's team remain on fifth position as they now have 15 points from 10 games they have played this season.
📷: FCB Nyasa Big Bullets media
Its true
"POMPANO TIKHALA TIMU YOTI ANTHU ATIKAMBA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake tsopano ikubweramo mmene amafunira ndipo posachedwa ikhale timu imene anthu atayikambe kuti ikuzizwitsa matimu ena mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati wakhutira ndi zotsatira za masewerowa poti masewero akuvuta mu ligi ya chaka chino.
"Ndakhutira ndi point imodzi chifukwa mapointsi akuvuta kupeza mu ligi ya chaka chino nde ndithokoze anyamata chifukwa asewera mozipereka mpaka tapeza point imodzi sitingayichepetse ndi yambiri imeneyi." Anatero Mtetemera.
Iye watinso timuyi posachedwa ikhale yovuta kusewera nayo chifukwa izipanga zomwe anthu samayembekezera ndipotu anyamata ake akumamvera kwambiri zomwe iye akuwauza.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi asanu (15) pa masewero khumi omwe yasewera mu ligi.
"ZINAONEKA KU ZOKONZEKERA KUTI TIWINA" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wathokoza anyamata ake kamba kolimbikira kuti apeze chipambano pomwe timuyi imasewera ndi timu ya Civil Service United lamulungu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi zigoli za Christopher Kumwembe ndipo wati kulimbikira kunayambira ku zokonzekera ndipo amadziwa kuti Iwo awina.
"Zinaonekeratu mmene timakonzekera kuti tiwina chifukwa anyamata analimbikira kwambiri ndipo mmasewerowanso tiwathokoze anayikapo mtima mpaka tapeza zigoli zitatu, chipambano ichi ndi chofunikira kwambiri." Anatero Mwase.
Iye wayamikiranso Kumwembe pogoletsa zigoli zitatu mmasewerowa ndipo wati anyamata akamalimbikira amapeza phindu lochuluka poti watola ndalama zambiri.
Manoma tsopano ali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero Khumi (10) omwe yasewera mu ligiyi.
📷: Ark Tembo
"TAGONJA TOKHA POPEREKA ZIGOLI" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati timu yake yagonja ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers chifukwa choti apereka zigoli okha kutimuyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndipo wati zangowavuta poti anyamata ake ndi omwewo omwe akhala akuchita bwino ndi timuyi mmbuyomu.
"Tagonja tokha masewerowa chifukwa tinapeza mpata wabwino koyambilira koma tinaphonya kenako Wanderers inabweramo tayipatsa chigoli kenako tinazitolera tapereketsanso chigoli kenako chachitatu nde tibwerera tikakonza ndipo zikhala bwino." Anatero Makawa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi 14 pa masewero khumi (10) omwe yasewera mu ligi ya chaka cha 2024.
"VUTO NDI KUPEZA ZIGOLI BASI" - YASIN
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ikungoyenera kukonza kutsogolo kwawo ngati akufuna ayambe kuchita bwino ndikumapambana masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Mzuzu City Hammers ndipo wati mavuto awo onse wawaona ndipo akonza kuti timuyi iyambirenso kuchita bwino.
"Anali masewero abwino mwina vuto lomwe tilinalo ndi kutsogolo koma ationetsa mbali zomwe tikufunikira kukonza nde tibwerera kuti tikakonze mavutowa." Anatero Yasin.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) pomwe ili ndi mapointsi 6 pa masewero khumi (10) yomwe yasewera mu ligiyi.
"TIMAYENERA KUPAMBANA NDIFE TIMU YAIKULU PA BANGWE" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Elias Chirambo, wati sakuyenera kukhala wosangalala ndi kupeza point imodzi kamba koti akanika kugonjetsa timu yomwe ndi yaing'ono kwa iwo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Mpira ndipo wati mwayi waukulu kuti apeze chipambano koma mwayi awutaya okha.
"Anali masewero abwino kwambiri tasewera bwino koma taphonya mipata yochuluka ndipo timayenera kuwina chifukwa timasewera ndi timu yaing'ono mwina tinavutika chifukwa anyamata athu omwetsa zigoli anavulala komabe sine wosangalala chifukwa timayenera kuwina." Anatero Chirambo.
Timuyi taphonya mwayi wofika pa nambala yachiwiri mu ligi ndipo ili pa nambala yachinayi mu ligi ndi mapointsi 17 pa masewero khumi (10) omwe yasewera mu ligi.
"NDIKUFUNIKA KUTI NDIKONZE MALO ONSE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose wati mu masewero ake oyamba waphunzira ndikuona mavuto ochuluka kwambiri omwe akuyenera kukonza kuti timuyi iyambirenso kuchita bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya MAFCO ndipo wati akufunikira kuti akonze mmalo onse komanso kuchotsa zibwana mwa osewera ena zomwe sizimafunikira posewera mu ligi ya TNM.
"Anali masewero abwino mwina nthawi zina timaoneka kuti titha kuchita bwino koma mavuto nde ndi ambiri kwabasi, mmasewero anga oyamba koma ndaona zambiri zofunika kukonza kuyamba kumbuyo paliponse nde ndikonza zonsezi." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 15 mu ligiyi pomwe yatolera mapointsi okwana asanu okha (5) pa masewero 15 omwe yasewera.
"TIYESETSA KUTI TIZICHITABE BWINO" - MZUNGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Jimmy Mzunga, wati ndi wokondwa poti timu yake ikuchita bwino ndipo ayesetsa kuti azigwiritsa ntchito mipata yomwe azipeza kuti azipeza zipambano.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa United 2-0 ndipo wati wathokoza osewera ake potsatira zomwe Iwo amawauza mmasewerowa.
"Anali masewero abwino tithokoze osewera athu kuti asewera bwino tapambana ndipo tiwalimbikitsabe kuti mwina tizichitabe bwino." Anatero Mzunga.
MAFCO tsopano ili pa nambala yachikhumi mu ligi pomwe yatolera mapointsi Khumi ndi awiri (12) pa masewero khumi (10) omwe yasewera.
"ZOMWE TIMANGOMVA ZAKU MULANJE TAZIONA" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya wati timu yake yakanika kupeza chipambano kamba koti zomwe anauzidwa kuti oyimbira amakondera timu ya FOMO waziona yekha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anabwenzetsa nthawi yothaitha kuti masewero athere 1-1 ndipo wati oyimbira anatenga mbali kuti timu ya FOMO izichita bwino mmasewerowa.
"Sindikumvetsa kuti zakhala bwanji kuti masewero athere chonchi chifukwa osewera asewera bwino ndipo anatsatira zomwe tinawauza koma mwina tinabwerera kumbuyo kwambiri nde anzathu amatha kubwera ndi mpira komabe oyimbira amawathandizira mmasewerowa zomwe ndinkangomva kuti zimachitika kuno." Anatero Bunya.
Timu ya Dedza Dynamos ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi awiri (12) pa masewero khumi omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Links
"WE ANTICIPATE A GOOD MATCH" - MWASE
Mighty Mukuru Wanderers interim coach, Meke Mwase, said he expects that his boys will rally against Civo United on Sunday as they were responding well during training.
Mwase said this ahead of the match on Sunday at the Kamuzu Stadium and said his boys are on high molare waiting to collect maximum points in the match.
"We had a very good week where we trained with our boys and they responded well, we anticipate a good game and we will fight for a win on Sunday." Said Mwase.
He further confirmed that all of his boys are available for the game as their are no injuries in his camp.
The Nomads are on position number 4 in the TNM Super League as they have 15 points from 9 games after recording four wins, three draws and two defeats.
Photo credit: Ark Tembo
PASUWA EXPECTS A TOUGH CRECK SPORTING CLUB
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Kalitso Pasuwa, said he expects another tough match against rookies Creck Sporting Club saying the team is fully motivated making them to be a tough opponent.
Pasuwa said this ahead of their meeting on Saturday and said his team got an important lessons in their last match after they lost to Silver Strikers as the youngsters experienced the pain of a loss and also to learn how to bounce back.
"In Football there are three results, you saw it in the last game we have a lot of youngsters who are just growing up, they have to see how a defeat pains and how to come back from a defeat. We can't say we were happy with the loss but they have to feel the pain of the defeat." Said Pasuwa.
He further said fans reactions after the loss also disturbed the players but demand the coaches to encourage the boys to put heads up geared for the next challenge.
The People's team sits on position 5 with 14 points from 9 games
CHESTER, MBULU HELP COSTA DO SOL MOVE TOP IN MOZAMBIQUE
Malawian attackers, Richard Mbulu and Yamikani Chester, were starters as Costa do Sol beat Ferroviario de Nampula 0-1 away to jump into the top spot in the Moçambola League in Mozambique on Saturday.
The visitors scored a goal by Zambian midfielder, Chisala, on 13th minute in the first half and that goal was enough to win the points.
Meanwhile, Lloyd Njaliwa was s second half substitute in the match while Chikoti Chirwa missed the match.
Costa do Sol sits now top with 20 points from 9 games this season, tying points with Black Bulls which has played 8 games and trail by a goal in the goal difference.
"MANOMA ASADZATENGE MIYALA LAMULUNGU" - MALUNGA
Mkulu wa masapota oyimba ku bwalo la zamasewero mdziko muno wa Mighty Mukuru Wanderers, Yonah Malunga, wapempha masapota atimuyi kuti afike pa bwalo la Kamuzu mwaunyinji kuti akaonere timu yawo yomwe ikumenya mwachizungu.
Iye wayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Civil Service United pa bwaloli ndipo wati timu yawo ikapambana poti ili bwino kwambiri komanso masapota asatenge miyala.
"Mkulu wanga Manoma sakupweketsa tikuwina masewero amenewa chifukwa Manoma alibwino kwambiri, masapota abwere adzaone mmene ikumenyera, akumenyatu mwachizungu ndipo asatenge miyala tidzavine, ine Yonah 1 Mpinganjira ndikhalanso konko." Anatero Yonah.
Timu ya Wanderers ili pa nambala yachinayi mu ligi pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi asanu (15) pomwe yapambana kanayi, kufanana mphamvu katatu ndi kugonja kawiri.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr 📷: MH photography
Mphunzitsi wakale watimu ya Flames, Meke Mwase, wati akufuna ndalama zokwana K1.5 billion kuti ikhale chipepeso chake kuchokera ku Football Association of Malawi kamba komuchotsa ntchito mosatsata malamulo.
Iye wafotokoza izi pomwe mlandu wake ukumvedwa ndi khothi limene limayang'ana za milandu ya ntchito ku Blantyre.
Source: Garry Chirwa (Weekend Nation) ?MH photography
MUNTHALI NEARS KB LOAN MOVE
Brighton Munthali could be moving to Kamuzu Barracks on loan from Blue Eagles after returning from South Africa where his loan contract at Black Leopards has expired and no effort have been put to renew it despite assurance from the Motsepe Foundation Championship side.
According to one of the country's publications, Dryborne Malawi, the deal is almost done as it awaits a signature from one of the elite persons at the Area 30 based side.
"He is about to join Kamuzu Barracks and everything is done, what is left is one of the bosses at Area 30 to sign the deal." Wrote Dryborne.
It is rumoured that he will replace on of the goalkeepers at the team who is leaving the country for peace keeping mission in DRC soon.
Munthali has opted for a move to safeguard his place at Flames because Blue Eagles plays in the Chipiku Stores Central Region Football League which is the second tier League in Malawi.
Source: Dryborne Malawi Sports news
"KUIMA KWA LIGI KUSOKONEZA MATIMU ENA" - MITAMBO
Katswiri wozukuta nkhani zamasewero mdziko muno, Justice Mitambo, wati kuima kwa masewero kwa masabata pafupifupi atatu kukhudza matimu amu TNM Supa ligi pomwe omwe amachita bwino akhonza kulowa pansi.
Iye amayankhula patsogolo pa kuyambiranso kwa masewero mdziko muno atayima kamba koti Flames imasewera masewero opitira ku World Cup ya 2026 komanso polira maliro a anthu asanu ndi atatu omwe anamwalira pa ngozi ya ndege.
Iye wati molalo ya matimu omwe amachita bwino ngati Silver Strikers, Mzuzu City Hammers komanso Kamuzu Barracks itha kulowa pansi pomwe ena atha kukonzanso zolakwika zawo.
"Molalo omwe unalipo kwa matimu omwe anayaka moto tisanapite ku tchuthi sungakhale chimodzimodzi pokhapokha aphunzitsi komanso akuluakulu awalimbikitse. Tinaona Silver Strikers itagonjetsa Jenda United ikuchokera kogonjetsa FCB Nyasa Big Bullets molalo umenewu utha kukhala pano wazizira."
"Matimu ngati Mzuzu City Hammers komanso Kamuzu Barracks san
"TIKUYANG'ANA KUTI TIKAPHWETSE MPHAMVU ZA BULLETS" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati masewero omwe akusewera ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets sakhala ophweka poti Bullets ndi timu yabwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo la Civo ndipo wati zoti Bullets inagonja ndi Silver Strikers zilibe ntchito poti timu iliyonse ndi yamphamvu koma ayesetsa kuti athetse mphamvu za Bullets.
"Inde tikuchokera kopambana ndipo iwo anagonja koma zilibe ntchito chifukwa timu iliyonse ndi yabwino mu ligiyi ubwino wake matimu onse tikudziwa mmene amamenyera, Silver komanso Bullets ndipo tingoona mmene tingaphwetsere mphamvu zawo komanso pomwe Ife tafooka tikwere." Anatero Nginde.
Iye watinso akhale ndi maphunziro ena omwe awakonzekeretse maganizidwe a osewera kuti asakhale obalalitsa pomwe akulowa mmasewero amenewa.
Timu ya Creck ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 14 pa masewero 9 pomwe yapambana kanayi,
BANGWE ALL STARS DUO LEAVE CLUB
Bangwe All Stars defensive duo of Sugzo Mwakasinga and Eric Atsigah have all left the club after staying for two months at the team.
Mwakasinga has terminated his contract and will look for another team while Atsigah is reported to have found a place at Intercontinental FK in Sweden.
On Thursday, Atsigah posted s photo which showed that he is currently in Kenya.
The two players joined the team when the 2024 season was about to commence all from Karonga United.
Source: Twaha Chimuka
"ADZAKHALA MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos akhale ovuta kwambiri chifukwa sanganame kuti ayidziwa poti iye anali kale komweko chaka chatha.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati iwo akonzeka kuti achite bwino pa masewerowa.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti Dedza Dynamos ndi timu yabwino koma tikukonzekera kuti tidzatenge chipambano pa masewerowa. Ndi timu yosiyana ndi ndi yomwe ndinali nayo, ndi nthawi ina iyi komanso masewero ena nde tingokonzekera kuti tipambane." Anatero Chirwa.
FOMO ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) ndi mapointsi khumi (10) pa masewero asanu ndi anayi (9) mu ligi ya chaka chino.
"SILVER SILI MOYESA TIKALIMBE" - ABAMBO
Mwini wake watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Robin Alufandika, wati ochemerera atimuyi avale zilimbe pomwe akukumana ndi timu ya Silver Strikers poti Mabanker alibwino kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali lolemba pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yawo inali ndi nthawi yokonza mwina ndi mwina komabe ndi Silver ndi masewero ovuta.
"Maso ndi maso maso ndi maso ndi Ma Banker koma zomwe zinachitike kumeneko ndi zomwezo. Masapota avale zilimbe chifukwa Silver sili moyesa." Anatero Abambo.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi 11 pa masewero 9 omwe yasewera pomwe yapambana katatu, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja kanayi.
SALIMA NDI WILLARD ACHIRA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti anyamata awiri, Chikumbutso Salima komanso Frank Willard, apezeka nawo pa masewero omwe timuyi isewere ndi Creck Sporting Club lamulungu pa bwalo la Civo.
Mphunzitsi watimuyi,. Kalitso Pasuwa, watsimikiza za nkhaniyi pomwe amafotokoza za osewera omwe akadali ovulala komanso omwe achira.
Salima anavulala mu sabata yachiwiri ya ligi ya chaka chino pomwe timuyi inkasewera ndi Mighty Waka Waka Tigers komwe Willard anavulala chaka chatha.
FOUR SUPER LEAGUE PLAYERS JOIN PRISON SERVICE TRAINING
TNM Super League sides, Premier Bet Dedza Dynamos and Mighty Waka Waka Tigers, have all suffered a huge blow after the departure of two players from each team to join the Malawi Prison Service.
According to one of the country's journalists, Twaha Chimuka, Tigers duo, Iven Mwakapenda and Bright Mtondagowa and two defenders from Dynamos, captain Justice Chihoma and Kondwani Kathumba, will join the service.
"Mighty Tigers midfield duo of Iven Mwakapenda and Bright Mtondagowa, Dedza Dynamos Captain Justice Chihoma and Kondwani Kathumba are expected to join Malawi Prison Service." Wrote Chimuka.
Meanwhile, Mwakapenda, Mtondagowa and Kathumba will join the service June 20 while Chihoma will join the service training on 26 June 2024.
Photo credit: MH Photography
NYONI WACHIRA KU SILVER
Katswiri wosewera mmbali ku timu ya Silver Strikers, Duncan Nyoni, tsopano wachira pomwe akuyembekezeka kupezeka lolemba likudzali pomwe Silver Strikers ikukumana ndi Mighty Waka Waka Tigers pa bwalo la Kamuzu.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi pomwe amapereka ndandanda wa osewera omwe akadali ovulala kutimuyi lachinayi ndipo wati anyamata atatu ena avulalanso kuonjezera pa ena omwe analipo kale.
Charles Chipala komanso Zebron Kalima sapezeka Kwa masabata awiri kamba kovulala ndipo Tatenda M'balaka sapezekanso sabata ino.
Koma nkhani yabwino ndi yoti Adiel Kaduya ndi Atusaye Nyondo ayamba zokonzekera zawo lachiwiri sabata ya mawa pomwe tsopano achira Malo omwe anavulala.
Silver ili pa nambala yoyamba mu ligi ndi mapointsi 25 pa masewero asanu ndi anayi (9) ndipo ikusiyana ndi yachiwiri mapointsi asanu ndi awiri (7).
Malawi National Football team has dropped points from 1141 to 1138 in the latest World FIFA rankings but have maintained their 125 position in the world.
This has been known in the latest rankings released by the World's Football governing body on Thursday.
The Flames have played two games this month, beating lowly ranked Sao Tome and Principe 3-1 before suffering a 1-0 defeat over Equatorial Guinea in the 2026 FIFA World Cup Qualifiers.
CHITIPA HIRE NYAMBOSE
Chitipa United has announced that they have hired former Mighty Tigers head coach, Christopher Nyambose, as the head coach for the team.
The team has made the announcement via their Facebook page on Thursday saying the coach has penned a one year deal with last season's most improved team.
"We are excited to announce the appointment of our new coach, Christopher Nyambose. With extensive experience and a passion for excellence, Nyambose is set to lead our team for a period of a year." Wrote the team.
He has replaced McNebert Ogrieve Kazuwa who resigned weeks ago. He also resigned in the third week of this season at Bangwe All Stars and stayed with no team.
BRIGHTON MUNTHALI WABWERERA KU BLUE EAGLES
Wosewera wotchinga pagolo kutimu ya Flames, Brighton Munthali, wabwerera kutimu ya Blue Eagles ndipo wayamba zokonzekera ndi timuyi kutsatira kutha kwa mgwirizano wa ngongole ku timu ya Black Leopards.
Munthali wafika mdziko muno kutsatira kutha kwa ligi ya Motsepe Foundation Championship ku South Africa ndipo mgwirizano wake unatha pa 20 June 2024 omwe ndi lero.
Katswiriyu ali ndi mgwirizano ndi Blue Eagles mpaka kufika mu chaka cha 2025 ndipo azisewera mu ligi ya Chipiku Stores ya chigawo chapakati ndi timuyi.
Masewero ake oyamba atha kukhala pakati pa Blue Eagles ndi Ekas Freight Wanderers omwe akumane mu chikho cha FDH Bank Cup.
CHITIPA EYE KAJAWA AS HEAD COACH
Chitipa United are currently talking to former Karonga United head coach, Trevor Kajawa, to become the coach and help things get settled at the team.
According to the information established by this publication, the team has seen Kajawa as a suitable candidate for a permanent job at the team as he also turned out Karonga United's misfortunes last season.
The Coach is currently with Lunzu Soccer Rangers after leaving Karonga United in the second week of the TNM Super League season but he will open to return to the North.
Meanwhile, Gift Nathaniel Mkamanga is the interim Coach who replaced Macnebert Kazuwa while Wakisa Munkhondiya is the interim deputy coach who replaced Elvis Kafoteka.
BULLETS YAKANA CECAFA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yakana pempho lokasewera mu mpikisano wa CECAFA Kagame Cup kamba koti ali ndi masewero ochuluka kwambiri.
Mkulu woyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, watsimikiza za nkhaniyi kunena kuti atakambirana awona kuti masewero awachulukira nde ndi kwabwino kusamala umoyo wa osewera.
Timuyi ndi imodzi mwa matimu atatu omwe anayitanidwa ndipo TP Mazembe yaku DRC nayo yakana poti osewera ali ku tchuthi pomwe ligi yawo inatha.
Matimu a Simba SC komanso Young Africans athanso osasewera kamba koti alinso ndi masewero ochuluka kwambiri.
Kupatula TNM Supa ligi, Bullets iseweranso mu zikho za FDH Bank, Castel Challenge, Airtel top 8 komanso mu CAF champions league.
KHUDA'S RICHARDS BAY STAYS IN SA TOP FLIGHT LEAGUE
Malawian forward, Khuda Muyaba, played for 23 minutes as Richards Bay FC thumped Baroka FC 4-0 to retain their place in the DSTV Premiership after finishing top in the Promotion and Relegation playoffs on Wednesday afternoon.
The team needed just a point going into the game in order to avoid relegation and scored two first half goals through Somila Ntsundwana on 37 minutes and Sanele Barns on 42nd minute to set sights clear back in the League.
Ntsundwana added third on 62nd minute before Khuda Muyaba was introduced for Yonela Mbuthuni on 67th minute and Lwandile Mabuya scored another on 85th minute.
Muyaba has now finished his five months contract with the team and he can stay at the team after they were banned from signing new players which can force them keep the 2019 Golden boot winner in the TNM Super League.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr.
NKHAKANANGA AKAYIMBIRA COSAFA
Woyimbira wa mdziko muno, Godfrey Nkhakananga, wasankhidwa kuti ayimbire nawo masewero a mpikisano wa chaka chino wa COSAFA Cup womwe uchitikire ku South Africa kuyambira pa 26 June mpaka pa 7 July.
Nkhakananga wasankhidwa mu la oyimbira a mmayiko osiyanasiyana kuti akayimbire mpikisanowu pamodzi ndi Pondamali Tembo yemwe ndi wothandizira kwa oyimbira pomwe ena ndi a mmaiko a Zambia, Zimbabwe, Seychelles, Angola, Mauritius, Botswana, South Africa, Eswatini ndi ena.
Sabata ziwiri zapitazo, Nkhakananga, anakayimbiranso masewero a mpikisano wa World Cup pakati pa ma timu a Djibouti ndi Sierra Leone ku Morocco.
Timu ya dziko lino siyisewera nawo ku mpikisano wa COSAFA kamba koti anatulukamo kuti akulira maliro a Dr Saulos Klaus Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.
BULLETS YAPEREKA NDALAMA KU SILVER
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yapereka ndalama zomwe zigwire ntchito kukonzetsa magalasi a galimoto ya timu ya Silver Strikers yomwe inagendedwa pomwe matimuwa amakumana mwezi watha.
Izi zachitika lachitatu masana pomwe mbali ziwirizi zinagwirizana kuti Bullets ikonzetsa bus imeneyi poti ochemerera awo ndi omwe anaphwanya magalasiwa pa bwalo la Kamuzu.
Timu ya Bullets inayendera mabanker kumakambirana mmene zinthu zawo zaonongekera ndipo Mapale analonjeza kukonza bus yawoyi.
Masapota a Bullets anayamba kugenda kutsatira kuti Chinsisi Maonga anagoletsa chigoli cha Silver mu mphindi yakumapeto ndipo timuyi ili ndi milandu iwiri yomwe ikuyankha ku bungwe la SULOM.
MWAUNGULU, LANJESI NDI CHAZIYA ANYAMUKA MU JULY
Osewera atatu amdziko muno, Patrick Mwaungulu, Lanjesi Nkhoma komanso Lawrence Chaziya, akanika kunyamuka posachedwapa ndipo anyamuka mwezi wa mawa kamba ka zifukwa zina.
Anyamatawa akumana ndi vuto loti omwe amayeza osewera kutimu ya TP Mazembe yaku DRC ali pa tchuthi komanso zipangizo zoyendera zavuta kaye koma mbali zonse zitha pa 10 July 2024.
Yemwe akuyendetsa kuchoka kwa osewerawa kupita kutimuyi, Felix Ngamanya watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati akati apite padakali panopa azikangokhala.
"Kuti osewerawa akayezedwe pamafunika dotolo komanso oyang'ana za mafupa kuti akakhalepo koma tsopano onsewa ali pa tchuthi mpaka pa 10 July nde mpake sitinanyamuke. Takumanso ndi vuto la zitupa zoyendera zomwe zachedwerako nde zonsezi zatiyimitsa kaye." Anatero Ngamanya.
Mgwirizano wapakati pamatimuwa utha ngati osewerawa angakhonze kuyezedwa kwa zachipatala ndipo adzasayina migwirizano yawo kutimuyi. Mwaungulu ndi Nkhoma amasewera FCB Nyasa
CHAWINGA WANTED MUCH IN EUROPE
UEFA Champions League finalists, Olympic Lyon, are reported to be chasing for the signature of Malawi's captain Tabitha Chawinga.
The player was in blistering form in the just ended season as she netted 19 goals and 10 assists in the D1 Arkema with PSG Women.
Meanwhile, PSG are also working hard to permanently sign Chawinga who has five months left at her Chinese Side, Wuhan Jiangda.
The player is also earning interests from Italy, Spain and English teams.
Osewera pakati kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Lloyd Aaron, wasankhidwa kuti ndiye wasewera mwapamwamba mu mwezi wa May kuposa osewera aliyense kutimuyi.
Izi zadziwika lachiwiri pomwe timuyi yalengeza kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook.
Iye anali osewera wofunikira kwambiri komwe anayithandiza kwambiri timuyi pomwe imasewera mmasewero awo osiyanasiyana mu ligi ya TNM mu mweziwu.
WELCOME BACK SPORTS IN MALAWI
The Malawi National Council of Sports has announced the resumption of different disciplines of Sports after its suspension last week.
The Association arrived at the decision after the burial of the State Vice president, Dr Saulos Klaus Chilima, who died tragically in a plane crash on Monday, 10 June 2024.
Meanwhile, the Association has communicated that people should continue paying respect to the departed souls in the games as the mourning period is not yet over.
All the tournaments in the country suspended their games following the Association's declaration and that also led to Flames' withdrawal from the COSAFA Cup of this year.
NEWS
Former Real Madrid defender, Sergio Ramos has left Sevilla after spending just one season.
The player is now a free agent and will be looking for a new team.
Source: Fabrizio Romano
BULLETS SINAPANGEBE CHIGANIZO CHOKASEWERA CECAFA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikulingalirabe ngati isewere nawo mu mpikisano wa CECAFA Kagame Cup kamba koti sanayankhebe pempho lomwe okonza mpikisanowu anawatumizira kuti akasewere nawo.
Izi zokhudza patamveka malipoti kuti mphunzitsi watimuyi, Kalitso Pasuwa, wapempha kuti timuyi isapiteko kamba koti masewero awachulukira zomwe zikhudze kuchita bwino kwa timu komanso thanzi la osewera.
Mpikisanowu ukuyembekezeka kuyamba pa 6 July 2024 ndipo matimu a Red Arrows yaku Zambia, TP Mazembe ya ku DRC ndi enanso mwa omwe anayitanidwa.
Kupatula masewero amu TNM Supa ligi, timuyi iseweranso mu FDH Bank, Castel, Airtel Top 8 komanso mu CAF champions league.
📷: MMH photography