"NDIKUFUNIKA KUTI NDIKONZE MALO ONSE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Christopher Nyambose wati mu masewero ake oyamba waphunzira ndikuona mavuto ochuluka kwambiri omwe akuyenera kukonza kuti timuyi iyambirenso kuchita bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya MAFCO ndipo wati akufunikira kuti akonze mmalo onse komanso kuchotsa zibwana mwa osewera ena zomwe sizimafunikira posewera mu ligi ya TNM.
"Anali masewero abwino mwina nthawi zina timaoneka kuti titha kuchita bwino koma mavuto nde ndi ambiri kwabasi, mmasewero anga oyamba koma ndaona zambiri zofunika kukonza kuyamba kumbuyo paliponse nde ndikonza zonsezi." Anatero Nyambose.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 15 mu ligiyi pomwe yatolera mapointsi okwana asanu okha (5) pa masewero 15 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores