SALIMA NDI WILLARD ACHIRA KU BULLETS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti anyamata awiri, Chikumbutso Salima komanso Frank Willard, apezeka nawo pa masewero omwe timuyi isewere ndi Creck Sporting Club lamulungu pa bwalo la Civo.
Mphunzitsi watimuyi,. Kalitso Pasuwa, watsimikiza za nkhaniyi pomwe amafotokoza za osewera omwe akadali ovulala komanso omwe achira.
Salima anavulala mu sabata yachiwiri ya ligi ya chaka chino pomwe timuyi inkasewera ndi Mighty Waka Waka Tigers komwe Willard anavulala chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores