"TAGONJA TOKHA POPEREKA ZIGOLI" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati timu yake yagonja ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers chifukwa choti apereka zigoli okha kutimuyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndipo wati zangowavuta poti anyamata ake ndi omwewo omwe akhala akuchita bwino ndi timuyi mmbuyomu.
"Tagonja tokha masewerowa chifukwa tinapeza mpata wabwino koyambilira koma tinaphonya kenako Wanderers inabweramo tayipatsa chigoli kenako tinazitolera tapereketsanso chigoli kenako chachitatu nde tibwerera tikakonza ndipo zikhala bwino." Anatero Makawa.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi 14 pa masewero khumi (10) omwe yasewera mu ligi ya chaka cha 2024.
📷: Ark Tembo
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores