"SILVER SILI MOYESA TIKALIMBE" - ABAMBO
Mwini wake watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Robin Alufandika, wati ochemerera atimuyi avale zilimbe pomwe akukumana ndi timu ya Silver Strikers poti Mabanker alibwino kwambiri.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe ali lolemba pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yawo inali ndi nthawi yokonza mwina ndi mwina komabe ndi Silver ndi masewero ovuta.
"Maso ndi maso maso ndi maso ndi Ma Banker koma zomwe zinachitike kumeneko ndi zomwezo. Masapota avale zilimbe chifukwa Silver sili moyesa." Anatero Abambo.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi 11 pa masewero 9 omwe yasewera pomwe yapambana katatu, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja kanayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores