"ADZAKHALA MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos akhale ovuta kwambiri chifukwa sanganame kuti ayidziwa poti iye anali kale komweko chaka chatha.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa lamulungu pa bwalo la Mulanje Park ndipo wati iwo akonzeka kuti achite bwino pa masewerowa.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti Dedza Dynamos ndi timu yabwino koma tikukonzekera kuti tidzatenge chipambano pa masewerowa. Ndi timu yosiyana ndi ndi yomwe ndinali nayo, ndi nthawi ina iyi komanso masewero ena nde tingokonzekera kuti tipambane." Anatero Chirwa.
FOMO ili pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) ndi mapointsi khumi (10) pa masewero asanu ndi anayi (9) mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores