"TIKUYANG'ANA KUTI TIKAPHWETSE MPHAMVU ZA BULLETS" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati masewero omwe akusewera ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets sakhala ophweka poti Bullets ndi timu yabwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo la Civo ndipo wati zoti Bullets inagonja ndi Silver Strikers zilibe ntchito poti timu iliyonse ndi yamphamvu koma ayesetsa kuti athetse mphamvu za Bullets.
"Inde tikuchokera kopambana ndipo iwo anagonja koma zilibe ntchito chifukwa timu iliyonse ndi yabwino mu ligiyi ubwino wake matimu onse tikudziwa mmene amamenyera, Silver komanso Bullets ndipo tingoona mmene tingaphwetsere mphamvu zawo komanso pomwe Ife tafooka tikwere." Anatero Nginde.
Iye watinso akhale ndi maphunziro ena omwe awakonzekeretse maganizidwe a osewera kuti asakhale obalalitsa pomwe akulowa mmasewero amenewa.
Timu ya Creck ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 14 pa masewero 9 pomwe yapambana kanayi,
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores