BRIGHTON MUNTHALI WABWERERA KU BLUE EAGLES
Wosewera wotchinga pagolo kutimu ya Flames, Brighton Munthali, wabwerera kutimu ya Blue Eagles ndipo wayamba zokonzekera ndi timuyi kutsatira kutha kwa mgwirizano wa ngongole ku timu ya Black Leopards.
Munthali wafika mdziko muno kutsatira kutha kwa ligi ya Motsepe Foundation Championship ku South Africa ndipo mgwirizano wake unatha pa 20 June 2024 omwe ndi lero.
Katswiriyu ali ndi mgwirizano ndi Blue Eagles mpaka kufika mu chaka cha 2025 ndipo azisewera mu ligi ya Chipiku Stores ya chigawo chapakati ndi timuyi.
Masewero ake oyamba atha kukhala pakati pa Blue Eagles ndi Ekas Freight Wanderers omwe akumane mu chikho cha FDH Bank Cup.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores