BULLETS SINAPANGEBE CHIGANIZO CHOKASEWERA CECAFA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikulingalirabe ngati isewere nawo mu mpikisano wa CECAFA Kagame Cup kamba koti sanayankhebe pempho lomwe okonza mpikisanowu anawatumizira kuti akasewere nawo.
Izi zokhudza patamveka malipoti kuti mphunzitsi watimuyi, Kalitso Pasuwa, wapempha kuti timuyi isapiteko kamba koti masewero awachulukira zomwe zikhudze kuchita bwino kwa timu komanso thanzi la osewera.
Mpikisanowu ukuyembekezeka kuyamba pa 6 July 2024 ndipo matimu a Red Arrows yaku Zambia, TP Mazembe ya ku DRC ndi enanso mwa omwe anayitanidwa.
Kupatula masewero amu TNM Supa ligi, timuyi iseweranso mu FDH Bank, Castel, Airtel Top 8 komanso mu CAF champions league.
📷: MMH photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores