BULLETS YAPEREKA NDALAMA KU SILVER
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yapereka ndalama zomwe zigwire ntchito kukonzetsa magalasi a galimoto ya timu ya Silver Strikers yomwe inagendedwa pomwe matimuwa amakumana mwezi watha.
Izi zachitika lachitatu masana pomwe mbali ziwirizi zinagwirizana kuti Bullets ikonzetsa bus imeneyi poti ochemerera awo ndi omwe anaphwanya magalasiwa pa bwalo la Kamuzu.
Timu ya Bullets inayendera mabanker kumakambirana mmene zinthu zawo zaonongekera ndipo Mapale analonjeza kukonza bus yawoyi.
Masapota a Bullets anayamba kugenda kutsatira kuti Chinsisi Maonga anagoletsa chigoli cha Silver mu mphindi yakumapeto ndipo timuyi ili ndi milandu iwiri yomwe ikuyankha ku bungwe la SULOM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores