"POMPANO TIKHALA TIMU YOTI ANTHU ATIKAMBA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake tsopano ikubweramo mmene amafunira ndipo posachedwa ikhale timu imene anthu atayikambe kuti ikuzizwitsa matimu ena mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati wakhutira ndi zotsatira za masewerowa poti masewero akuvuta mu ligi ya chaka chino.
"Ndakhutira ndi point imodzi chifukwa mapointsi akuvuta kupeza mu ligi ya chaka chino nde ndithokoze anyamata chifukwa asewera mozipereka mpaka tapeza point imodzi sitingayichepetse ndi yambiri imeneyi." Anatero Mtetemera.
Iye watinso timuyi posachedwa ikhale yovuta kusewera nayo chifukwa izipanga zomwe anthu samayembekezera ndipotu anyamata ake akumamvera kwambiri zomwe iye akuwauza.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi asanu (15) pa masewero khumi omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores